Ulemu ndi chinthu chofunika kwambiri chimene aliyense ayenera kuchidziwa. Kupereka ulemu ndi lamulo la m’Baibulo. Ulemu ndi wofunika kwambiri mu ubale wako ndi Mulungu.
Ulemu ndi wofunika kwambiri mu ubale wako ndi mneneri wako, abusa ako, mwamuna wako ndi ena onse amene ali ndi udindo pa iwe. Ukasapatsa ulemu kwa amene ulemu wake uyenera kuperekedwa, sudzakhala ndi ubale woyenera ndi anthu ena ena. Ili ndi buku la malangizo a moyo.
M’bukuli mudzaphunzitsidwa mmene mungalemekezere munthu, zizindikiro za kusalemekeza, mphotho za ulemu ndi zina zambiri. Bukuli lili ndi makiyi okuthandizani kusunga ndi kuteteza maubale anu ofunika. Musapezeke osakwanira pankhani ya ulemu!

Reviews
There are no reviews yet.