Kodi Mumakonda Ambuye? Limeneli ndi funso lofunikira! Ambuye wathu, Yesu Khristu, anafunsa Petro, “Petro umandikonda Ine?” Chifukwa chiyani chikondi chanu pa Mulungu ndi chinthu chimene tiyenera kukambilana? Yesu akuti lamulo lalikulu ndilakuti “mumukonde Ambuye Mulungu wako, ndi Mtima wako wonse, moyo wako wonse ndi malingaliro ako onse.”
Nthawi zina, pamakhala nyengo zina zimayikidwa pamodzi komanso kuperekedwa kwa inu ndi Ambuye zimene zili mayesero, mayesero otsimimizira umboni wanu pa Ambuye. Ngati mumakonda Ambuye, tsimikizirani pa kupambana mayesero a chikondi!
Bukhu lina lodabwitsa la mlembi wotchuka, Dag Heward-Mills, limene likupangitseni kuganiza komanso kudzifunsa nokha funso lofunikira lonse “Kodi ndimakondadi Ambuye?”

Reviews
There are no reviews yet.