Dag Heward-Mills ndi wolemba wa mabuku ambiri, kuphatikizapo logulitsidwa kwambiri “Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika”. Ndi woyambitsa wa Mipingo ingapo yochokera ku Lighthose ndi matchalitchi zikwi zitatu.
Dag Heward-Mills, mvangeli wadziko lonse, amatumikira mu misonkhano ya machiritso mu maiko komanso misonkhano ya atsogoleri padziko lonse. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa
www.daghewardmills.org.
-
Baibulo ladzaza ndi mawu olimbikitsa kuti tizipemphera: "Zonse mu pemphero! Kukhala mukupemphera nthawi zonse! Anthu ayenera nthawi zonse kupemphera! Pempherani nthawi zonse! Pempherani osasiyasiya!" M'bukuli lodabwitsali, "Zonse mu pemphero, palibe popanda pemphero", mudzayamba ulendo wokuphunzitsani njira ndi makhalidwe a moyo wa pemphero wa Yesu Khristu. Ngati Yesu ankapemphera, ndiye kuti ine ndi iwe tiyenera kupemphera kwambiri. Chilichonse m'moyo mwathu chingakwaniritsidwe kudzera mu pemphero ndipo palibe chimene chingakwaniritsidwe popanda pemphero. Moyo wako wa pemphero udzakhala wosangalatsa kwambiri ukatha kuwerenga bukuli losangalatsa! -
Chinthu chimodzi chokha chimadza kwa inu mukamva mawu akuti "M’busa" - nkhosa! Nkhosa ndi nyama zodalira zome zimafunikira abusa. M’busa ndi wotsogolera wosamalira komanso wachikondi kwa nkhosa. M'Baibulo, Mulungu amatitchula ife ngati gulu la nkhosa za Mulungu. Yesu adamuuza wophunzira Petro kuti adyetse nkhosa zake kuti atsimikizire za chikondi chake cha Mpulumutsi. Kukhala m'busa ndi ntchito yabwino kwambiri. Ndi chinthu chapamwamba kuitanidwa ndi Mulungu ndi kulembetsedwa mwa antchito Ake ndi kusamalira nkhosa. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutiitanira ife, akutilimbikitsa ndi kutiwonetsa ife momwe tingatengerepo nawo mbali pa ntchito yayikulu yosamalira anthu a Mulungu. Musati muzisiyidwe kunja kwa ntchito yabwino iyi yokhala m’busa! -
Baibulo limatiuza kuti tonse timalakwitsa- Abusa nawo amalakwitsanso. Kulakwitsa kumabwezeretsa m’mbuyo. Kulakwitsa kumalepheretsa kupita chitsogolo. Kodi ndi zolakwitsa ziti zimene abusa anu apanga? Kodi ndi chiyani chingakhale zolakwitsa zazikulu khumi zimene abusa amachita? Muli omasuka kuwerenga Bukuli ndi kuzindikira zolakwika zimene mungazichite ndi m'mene mungazipewere. Buku lofunikali lidzakhala mdalitso kwa inu ndi utumiki wanu. -
Kodi Chimachitika Ndi Chiyani Mukabadwa Mwatsopano? Mzimu wa Mulungu azabwera pa inu, komanso mumtima mwanu. Kenako mkati mwanu mudzabadwa kapena kupangidwanso. Mulungu amakupatsani mtima watsopano ndi mzimu zonse! Ndi mzimu wanu watsopano, mumakhala munthu watsopano kapena cholengedwa chatsopano. Mwakonzeka kukhala moyo watsopano. Moyo watsopanowu ndiwotheka chifukwa ndiwe munthu watsopano wamtima watsopano. Kubadwa mwatsopano ndikosavuta monga choncho. Anthu amafuna kuchita zinthu zovuta. Koma kubadwanso mwatsopano ndikosavuta! -
Lonjezo ili pa Yobu 8:7 : “Chingakhale chiyambi chako chinali chaching’ono, koma chimaliziro chako chidzachuluka ndithu” chikutisonyeza kuti Mulungu ali ndi cholinga cha kukula ndi kutukumuka kwa miyoyo yathu. Ndi dalitso lotani nanga kulowetsedwa m’zinsinsi zimene zidzatsogolera ku kukulitsa kwathu! Kupyolera mu zinsinsi zambiri zakukulitsa zovumbulutsidwa ndi wolemba, Dag Heward-Mills, tikuphunzira kuti kukulitsa kudzabwera kwa inu kupyolera mu zowawa, mndandanda wa nkhondo, kupambana ndi kulandira cholowa cha Mulungu. Tikuphunziranso kuti mutha kukulitsidwa mukamagwiritsa ntchito zinsinsi zakukulitsa za kusinkhasinkha, mbiri yakale, mabuku ndi nzeru. Kukulitsa kungathenso kubwera kwa inu kudzera mu nsembe ndi mphamvu zauzimu. Phunzirani zinsinsi zomwe zafotokozedwa m'bukhuli ndi kupindula ndi choonadi chake chodabwitsa. -
Moyo ungakhale wovuta kwa aliyense. Nthawi zambiri chomwe mukufuna kuti mugonjetse chomwe inu mwagwamo ndi nzeru. Nzeru ndi chinsinsi cha Mulungu chomwe chikuthandizeni inu kuwuka kuchokera nkulimbana ndikukhala chozizwitsa chamoyo. Mulungu wakuikani inu ku ulemerero. Chinsinsi cha Mulungu ndi nzeru ya Mulungu mu chinsinsi chomwe chaikidwa pa ulemerero ndi kukongola kwanu. Zibvumbulutso za bukhuli zikubweretsereni chigonjetso tsiku lililonse! Bukhu ili likupatseni chidziwitso ndi kupambana! -
Phunziro losangalatsa komanso lozama ili pa mutu wa “chikhulupiriro” lidzakopa wina aliyense yemwe cholinga chake ndi kukondweretsa Mulungu. Pakuti popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu, malemba amanena choncho. Ichi ndichifukwa chake bukuli ndilofunika kuwerengedwa ndi aliyense amene ali ndi chikhumbo chokondweretsa Mulungu. Ngati chikhulupiriro chinapangitsa Abrahamu kukhala bwenzi la Mulungu, ndiye kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri pa kuyenda kwathu ndi Mulungu. Bukuli ndi chuma chenicheni! Dziwani zinsinsi zofunika kuti muyende ndi kukhala ndi moyo mwa chikhulupiriro. Tsegulani zinsinsi za chikhulupiriro zomwe mukuzifunikira kuti muchite zinthu zosatheka m’moyo wanu! -
Bola Mulungu akutipatsa moyo, tili ndi mwayi wochita zinthu zazikulu. Lero uli ndi mwayi woyesa kuchita zinthu zazikulu za Mulungu. Osachepera, yesa! Panga kuyesa! Ili ndi buku lomwe lidzakulimbikitsa kuti ukhale wabwino kwambiri, mmene Mulungu anakupangira kuti ukhale. Dzipatse chiganizo choyesa kuchita zinthu zazikulu za Mulungu tsiku lililonse, ndipo udzadabwa ndi zimene udzatha kuchita mwa chisomo cha Mulungu. Zopambana zazikulu zikukudikirirani pamene umafufuza mosamala zomwe zili m’bukuli ndi kuyesa kuchita chinachake chachikulu chifukwa cha Mulungu! Muzachita zopambana za Mulungu! -
Mzimu Woyera amafotokozedwa m’njira zambiri: monga mtsinje, monga madzi, monga mphepo, monga mafuta, monga blanketi, monga nkhunda, ndi zina zotero. Kuyenda mu kudzodzedwa ndi kuyenda limodzi ndi Mzimu Woyera m’njira zosiyanasiyana zimene Iyeyo amadzionetsera yekha. Zikuchitikireni kuti muzipeza Mzimu Woyera mkati mwanu, pamodzi nanu komanso pa inu! Ndikupemphera kuti muzilola dzanja lamphamvu la Mulungu likutsogolereni pamene mukungoyenda naye momasuka!