• Baibulo limatilangiza ife ku: "Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzakeyo" (Afilipi 2:4). M'bukhu la m'nthawi yakeli, Dag Heward-Mills akukuwuzani inu mupitirire kuganiza za inu nokha ndi kuganizanso za ena! Mukondenso ena! Muganizirenso ena! Musamalenso za ena! Mukhalenso chifukwa cha ena! Yesu anadza kudzatifera ife chifukwa Iye anaganiza za "ena". Ine ndikufuna kukhala kwambiri ngati Iye. Kodi inu mukufuna kukhala ngati Yesu?
  • Anthu ambiri amapereka maola ambiri akugwira ntchito ndi cholinga chimodzi chokha – kukhala olemera! Tsoka ilo, chuma chimawatha m'manja anthu ambiri pamene amalifuna molimbika kukhala olemera. Chifukwa chiyani? Chifukwa amafuna kungokhala olemera, pamene pali cholinga chapamwamba, choposa chuma, chimene Mulungu amafuna kuti uzigwirira ntchito. Bukuli likufotokoza zinthu zimene Baibulo limanena kuti uyenera kupereka moyo wako kuzochita zimenezo. M’malo mongogwira ntchito kuti ukhale wolemera, udzaphunzira kugwira ntchito chifukwa cha zinthu zapamwamba! Landirani masomphenya atsopano okhala dalitso kwa ena pamene mukuwerenga bukuli latsopano, lokopa chidwi, lolembedwa ndi Dag Heward-Mills!
  • Baibulo limatichenjeza mosapita m’mbali kuti zokhumudwitsa zidzafika kwa ife.  Izi zikutanthauza kuti padzakhala zochitika m'moyo chomwe sichingakusangalaseni ndikukukhumudwitsani. Kodi chenjezo limeneli limatikonzekeretsa mokwanira kuti tigonjetse pamene takhumudwitsidwa?  Kodi mungadzitetezere kuti musakhumudwe? Kodi mudzalola kuti kukhumudwitsa kukupangitseni kusakhulupirika chinthu chamtengo wapatali chotchedwa “kudalira”?  Bukhuli ndi bukhu lanu la mayankho ku mafunso owopsa awa. M’bukhu ili, Dag Heward-Mills akufotokoza zotsatira za zolakwa pa ife. Timaphunzira kuti zolakwa zimatipweteka ndi kutikwiyitsa, komanso kuti zolakwa zina zimakhala zovuta kuzikhululukira ndi kuziiwala. Bukhulinso ndi chida chophunzirira momwe tingagonjetsere zolakwa kuti tisakhale akapolo a kukhumudwa.
  • Mu bukhu lapamwambali, Bishop Dag Heward-mills amaphunzitsa za momwe chida cha kukhulupirika chimalimbikitsa kachitidwe ka mtsogoleri. Kugwiritsa ntchito baibulo, mbiri ndi zolemba, mutu uwu wapangidwa kukhala woyenera kwa wowerenga.
  • Bukhu iri ndi mphatso ina kuchokera ku cholembera cha Dag Heward-Mills kwa azitumiki onse amene atha kupeza nthawi yowerenga. Bukhuli lizayankha mafunso onse okhuzana ndi momwe mungakwaniritsire kukhala ndi ubale wabwino pakati pa atate ndi ana. Kudzera mu chiphunzitso cha bukhu limeneri, muzapewa themberero pa moyo wanu ndi kubweretsa kwanokha mdalitso. Atate ndi anthu apadera amene amakuza ana. Popanda atate sipazakhala ana kupitiriza utumiki ku mibadwo ina. Maitanidwe a Mulungu amakula kapena kufa ndi kuthekera kochitirana ndi atate. Werengani bukhu limeneri ndipo pewani themberero lokhuzana ndi kusalemekeza, kusamvera ndi kukhala ndi ubale woipa ndi atate.
  • Kudzikweza ndi poizoni wakupha amene waononga mtundu wa anthu mzaka zambiri. Chifukwa nkosatheka, kudzikweza kumakwaniritsa kupangitsa chionongeko chachikulu popanda kuonekera. Tingamenyane bwanji ndi chiopsezo chimenechi ku miyoyo yathu? Ndi katemera wa kudzichepetsa! Kudzichepetsa ndi chabwino chauzimu. Ochepa akwanitsa kulemba zokhudzana ndi chofunikira chauzimuchi. Mu bukhu latsopano losangalatsali, Dag Heward-Mills akuonetsera mitundi yobisika ya kudzikweza. Bukhu la mphamvu limeneri, lolembedwa ndi Mkhristu wovutika mzathu, likudalitsani ndi kukulimbikitsani inu kukuza kudzichepetsa konga mwana kwa Yesu Khristu.
  • Anthu opanduka samakumbukira zomwe zapangidwa kwa iwo ndipo nthawi zambiri amasankha kuiwala zinthu zina. Yudase sanakumbukire zimene Ambuye anamchitira, ndinso sanakumbukirenso zinthu zimene anaona ndi kumva kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake adakhala mtundu wa munthu amene tikumudziwa lero ngati ‘Yudase’. Kuthekera kokumbukira ndi chimodzi mwa zinthu zauzimu chomwe mtumiki atha kukhala nacho. Anthu amene samakumbukira, siwamba kuchita bwino. Iwo amalephera kufika mlingo wina. Bukhu lapaderali, pa mutu wosakambidwa kwambiriwu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kwa inu.
  • Ulemu ndi chinthu chofunika kwambiri chimene aliyense ayenera kuchidziwa. Kupereka ulemu ndi lamulo la m’Baibulo. Ulemu ndi wofunika kwambiri mu ubale wako ndi Mulungu. Ulemu ndi wofunika kwambiri mu ubale wako ndi mneneri wako, abusa ako, mwamuna wako ndi ena onse amene ali ndi udindo pa iwe. Ukasapatsa ulemu kwa amene ulemu wake uyenera kuperekedwa, sudzakhala ndi ubale woyenera ndi anthu ena ena. Ili ndi buku la malangizo a moyo. M’bukuli mudzaphunzitsidwa mmene mungalemekezere munthu, zizindikiro za kusalemekeza, mphotho za ulemu ndi zina zambiri. Bukuli lili ndi makiyi okuthandizani kusunga ndi kuteteza maubale anu ofunika. Musapezeke osakwanira pankhani ya ulemu!
  • “Mwina mmodzi mwa adani aakulu omwe mutha kukumana nawo ndi ‘woneneza pakati pa abale’.” Landirani chidziwitso chachikulu cha momwe chida chimenechi cha kuneneza chimadzera ndipo phunzirani za momwe mungachigonjetsere, pomwe mukuwerenga bukhu lapamwambali, lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Anthu amene amakusiya atha kukuwonongani. Palibe chimene chingalongosera kumva kwa kukhumudwa, kubalalika ndi nkhawa zimene zimadza pamene anthu akukusiyani. Bukhu ili lalembedwa kukuthandizani inu kulimbana ndi chiwonongeko chomwe chimadza pamene anthu akusiyani. Musanyengedwe. Kusiidwa sikwachilendo kwa inu ndi utumiki wanu. Ambiri ena avutika ndi zomwezo. Satana anali wopanduka woyamba ndipo akulimbikitsa opandukira onse kuyambira pamenepo. Ndi bukhu limeneri mu manja anu, muzachirimika ndi kulimbana ndi mzimu wa kusakhulupirika umene umadza ndi “iwo amene amakusiyani”.
  • Mipingo yadzadzidwa ndi onamizira angwiro amene amakhala osakhulupirika mwangwiro. Chida cheni cheni cha Satana chakhala chinyengo ndi kunamizira. Mtsogoleri amene sazindikira wonyenga azavutika chifukwa cha kusaona kwake.Kuopseza, chizolowezi ndi chisokonezo ndi mizimu yoipa imene imalimbana ndi azitumiki. Nthawi zambiri, anthu samadziwa chomwe chimalimbana nawo. Bukhu ili likakuthandizani inu kudziwa ndi kulimbana ndi mdani wamkati.
  • Yesu Khristu akuonetsera mfundo yodabwitsa yomwe ikutsogolera kuchita bwino ndi chuma. Iye amene ali nako kanthu azakhala nazo zambiri! Zikumveka mokondera! Koma, ichi ndi chilungamo chomwe chikuonetsedwa kwa ife tsiku ndi tsiku. Bukhuli likulongosola Lemba losamvetsetseka kwambiri iri. Muzalandira chidziwitso chachikulu ku zinsinsi za kuchita bwino pamene mukuwerenga bukhu latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.

Title

Go to Top