• Dr. Dag Heward-Mills, mtsogoleri wa Chikhristu wopambana, akuonetsa chimodzi mwa zinsinsi zake. “Ngati wina atandifunsa chomwe chinsinsi changa chachikulu cha ubale wanga ndi Mulungu chiri, nditha kunena, musaopa, kuti ndi mphamvu ya nthawi za chete yomwe ndimakhala nayo ndi Iye tsiku ndi tsiku.” Iwe waganiza kulemba bukhuli kuti inunso mukapindule kuchokera ku mphamvu ya nthawi ya chete.
  • “Ndingapemphere bwanji? Kodi ndipempherere chani? Kodi pemphero ndilodabwitsa chifukwa chani? Ndingapemphere bwanji kwa nthawi yaitali? Kodi Mulungu sakudziwa zomwe ndikufuna? Mapemphero anga ayankhidwadi?” Pezani mayankho a mafunso amenewa pomwe mukuwerenga bukhu lobwera panthawi yake lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Tonse timalindirira moyo waulemerero komwe kuzakhala "KULIBENSO THEMBERERO!" Ichi ndi chifukwa choti mmoyo timakumana ndi matsoka, kuzunzika kopitirira, utsiru, kusasangalala ndi kukhumudwa. Themberero limafotokoza bwino matsoka okumana nawowa omwe tikuwoneka kuti timakumana nawo. Tingazipewe? Pali njira yosakumanirana nazo? Bukhuli likakuthandizani inu kumvetsetsa matemberero ndi momwe mungazikhadzikitsire nokha kuti mukalandire mdalitso.
  • Bukhuli ndi chiongolero chapadera ku kumvetsetsa chipulumutso kudzera mwa Yesu Khristu. Mu bukhu la pamwambali, muzamvetsetsa momwe Yesu amakukonderani inu, momwe mungabadwire mwatsopano, momwe mungapewere kupita ku gehena ndi chomwe chimatanthauza kukhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu. Perekani bukhuli kwa wina aliyense ndipo azamvetsetsa zomwe zikutanthauza kupulumutsidwa kudzera mu mwazi wa Yesu Khristu.
  • Baibulo limayankhula za mitundu yambiri ya mwazi: mwazi wa mbuzi, mwazi wa nkhosa, mwazi wa nkhunda! Baibulo limatiuzanso kuti popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo. Ndiye kodi umodzi mwa mitundu iyi ungather kuchotsa machimo?yankho ndi ‘Ayi’ wotsindika. Ndiye ndi chani chingachotse machimo athu? Palibe, koma mwazi wa Yesu Khristu! Ndi mwazi wa Yesu wokhawo umene uli ndi mphamvu kukachotsa machimo athu ndi kutibweretsera chipulumutso. Mu bukhu lofunikira kwambiri limeri, muzapeza zilungamo zoyera kwambiri zokhuzana ndi mwazi wa Yesu Khristu. Mupeza momwe mwazi wa Yesu umaperekera moyo ndi momwe mwazi wa Yesu unapezera kufunikira kwake. Muzamvetsetsa chiyanjano cha pakati pa Mzimu Woyera ndi mwazi wa Yesu. Mulidi mphamvu mu mwazi wa Yesu!
  • “…Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe. KUTI NYUMBA YANGA IDZALE.” Luka 14:23. Kulira kwa Mulungu ndi kwakuti dziko lonse lipulumutsidwe, ndi kuti nyumba Yake-tchalitchi-lidzale! Kuchokera ku vumbulutso limeneri bukhu iri linabwera., “Mpingo Waukulu” lolembedwa ndi Bishop Dag Heward-Mills, m’busa wa umodzi mwa mipingo yaikulu kwambiri ku Ghana. Mpingo wanu ndi utumiki wanu sudzakhalanso chimodzi modzi mukawerenga bukhu lolimbikitsali!“Dr. Heward-Mills ndi wodzipereka kwa Ambuye Yesu Khristu ndi ntchito yotenga mbali pa kulalikira ku dziko lonse. Ndi mtsogoleri wamphamvu ndinso chitsanzo ku mautumiki onse, ndipo ife ku “Church Growth International”, ndife olemekezedwa kudziwa ndikumutcha Dr. Dag Heward-Mills mnzathu komanso wogwira naye limodzi ntchito mu kholola lalikulu mu minda ya padziko.” -Dr. Yonggi Cho Wamkulu, Church Growth International
  • Anthu ambiri samamvetsetsa za malo a mtengo wa dzindikila chabwino ndi choipa m`moyo mwathu. Nthawi zambiri timaganiza kuti unali mtengo qmwe unalipo kalekale munthawi ya Adamu ndi Eva. Timakhulupirira kuti mtengo umeneyo unali ndi zipatso za poizoni zoti ukangodya yemwe wadyayo amafa. Mwa tsoka, Adamu ndi Eva anadya za mtengowu ndipo anafa. Tikawerenga za nkhaniyi, timaganiza kwa ife, “zinali zomvetsa chisoni Adam ndi Eva kudya chipatso chakuphachi koma tithokoze sitidzaikidwa m`mayeselo ndi mtengo ngati umenewo”. Zachisoni, tikhala tikulimbana ndi mtengo umenewu ndi zipatso zake. Chomwe tiyenera kudziwa ndi chakuti za mtengo wa kudzindikira chabwino ndi choipa udakalipobe mpaka lero. Umagwira ntchito m`mayesero kwa ife chimodzimodzi m`mene unapangira nthawi ya Adamu ndi Eva. Umayimilira ngati njira ina ya kwa Mulungu.
  • Mau opatsa chidwi amenewa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi" analankhulidwa ndi Yesu Khristu pa gulu lake laling’ono la ophunzira khumi ndi awiri. Ambiri a ife timachitiridwa zowawa ndi mdierekezi chifukwa sitimadziwa momwe tingamuonetsera poyera kapenanso kukazindikira zintchito zake. Mu bukhu lodalitsika limeneli, mudzatulukira uchimo wa mdierekezi ndi kupanga chisankho cha kusayenda mmenemo. Zikhale kuti mau awa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi” asakhale akunenera pa inu!
  • Mu buku lopambanali, Dag Heward-Mills akusanthula zinthu zochitikadi mu utumiki masiku ano. Akukamba za zinthu zochitika zokhudza zachuma, ndale, kucheza ndi amuna kapena akazi komanso maubale mu utumiki. Bukuli ndi muuni wa makhalidwe otsatira mwambo pa mayitanidwe anu ndipo ndi buku lomwe mtsogoleri wachikhristu aliyense akuyenera kukhala nalo. Ndi lovomerezeka ku sukulu za Baibulo ndi kwa atumiki onse.
  • Bukhuli lizachiza kusweka mitima kwa ana aakazi! Mubukhu loyembekezerekali, akazi akulimbikitsika kulola nzeru ya Mulungu kuwathandiza iwo kugonjetsa zinthu zosatheka zambiri zomwe amakumana nazo. Mulungu adzakhuza moyo wanu ndi kulimbikitsa inu pamene mukulimva bwino bukhu lamphamvu latsopanoli maka maka kwa ana aakazi.
  • Mutha kukhala kuti munamvapo kuti ndi chinthu chachikulu kutumikira Ambuye; koma inu mutha kukhala kuti simunaganizire bwino momwe chili chabwino zedi kutumikira Ambuye Mulungu wathu. M'bukhu lapaderali la Dag Heward-Mills inu mukamvetsa kuti mtumiki wa Mulungu ndindani ndi momwe inu mungamutumikirire Ambuye. Mukadziwe mochita kusiyana pakati pa iwo amene amamutumikira Ambuye ndi iwo amene samutumikira Iye! Inu mukawerengedwe ndi iwo amene amamutumikira Ambuye!
  • Mukusirira kukhala odzozedwa? Mu bukhu la mbiri ili, Dr. Heward-Mills akugawana nafe ndondomeko zolandirira kudzoza. Bukhuli likakhala maka maka mdalitso kwa inu ndi utumiki wanu. Zindikirani ndondomeko mukufunikira kutenga kuti mukhale odzozedwa!

Title

Go to Top