Lonjezo ili pa Yobu 8:7 : “Chingakhale chiyambi chako chinali chaching’ono, koma chimaliziro chako chidzachuluka ndithu” chikutisonyeza kuti Mulungu ali ndi cholinga cha kukula ndi kutukumuka kwa miyoyo yathu. Ndi dalitso lotani nanga kulowetsedwa m’zinsinsi zimene zidzatsogolera ku kukulitsa kwathu!
Kupyolera mu zinsinsi zambiri zakukulitsa zovumbulutsidwa ndi wolemba, Dag Heward-Mills, tikuphunzira kuti kukulitsa kudzabwera kwa inu kupyolera mu zowawa, mndandanda wa nkhondo, kupambana ndi kulandira cholowa cha Mulungu. Tikuphunziranso kuti mutha kukulitsidwa mukamagwiritsa ntchito zinsinsi zakukulitsa za kusinkhasinkha, mbiri yakale, mabuku ndi nzeru. Kukulitsa kungathenso kubwera kwa inu kudzera mu nsembe ndi mphamvu zauzimu.
Phunzirani zinsinsi zomwe zafotokozedwa m’bukhuli ndi kupindula ndi choonadi chake chodabwitsa.

Reviews
There are no reviews yet.