• Ismerd meg ezt a kényszerítő erőt, amely hatékonnyá és gyümölcsözővé teszi az evangélizációt az ellenállás, a kifogások, a gyanakvás, a neheztelés, és más hasonló problémák ellenére is! Dag Heward-Mills könyve jobb léleknyerővé tehet téged, mint amilyen eddig voltál.    
     
  • Maitanidwe ku utumiki ndi maitanidwe ku utsogoleri. Kachi kena kudzera munjira zomveka bwino, Dr. Heward-Mills akulongosola mfundo zikulu zikulu zomwe zampanga iye kukhala mtsogoleri wa Chikhristu wopambana. Zilungamo zoonetseredwa muno zikalimbikitsani ambiri ku luso la utsogoleri.
  • Chuma cha kudzodza chili mwa odzodzedwa. Kudzoza sikosiyanitsidwa ndi munthu wodzozedwa. Kudzoza kuli mwa munthu wa Mulungu! Kudzoza kuli ndi munthu wa Mulungu! Kudzoza kuli pa munthu wa Mulungu. Bukhu latsopano ndi losangalasa la Dag Heward-Mills lisangalasa mitima ya iwo omwe akufunafuna kudzoza.
  • Kutsatira Mulungu ndi ulendo wosangalatsa wopeza zinthu. Kutsatira ndi kutengera anthu ena ndi luso lachikale lophunzirira lomwe Yesu Khristu anasankha ngati njira yaikulu yophunzitsira. M’malo mochita manyazi ndi njira yoyesedwa ndi nthawiyi, ndi nthawi yomvetsetsa kukongola ndi kudzichepetsa kwa luso la kutsatira. Mu bukhuli, muzapeza yemwe, chomwe ndi momwe mungatsatire moyenerera. Bukhu lopambana latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills lipereka luso la kutsatira malo ake oyenerera mu zokumana zathu za Chikhristu.
  • Chinthu chimodzi chokha chimadza kwa inu mukamva mawu akuti "M’busa" - nkhosa! Nkhosa ndi nyama zodalira zome zimafunikira abusa. M’busa ndi wotsogolera wosamalira komanso wachikondi kwa nkhosa. M'Baibulo, Mulungu amatitchula ife ngati gulu la nkhosa za Mulungu. Yesu adamuuza wophunzira Petro kuti adyetse nkhosa zake kuti atsimikizire za chikondi chake cha Mpulumutsi. Kukhala m'busa ndi ntchito yabwino kwambiri. Ndi chinthu chapamwamba kuitanidwa ndi Mulungu ndi kulembetsedwa mwa antchito Ake ndi kusamalira nkhosa. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutiitanira ife, akutilimbikitsa ndi kutiwonetsa ife momwe tingatengerepo nawo mbali pa ntchito yayikulu yosamalira anthu a Mulungu. Musati muzisiyidwe kunja kwa ntchito yabwino iyi yokhala m’busa!
  • “…Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe. KUTI NYUMBA YANGA IDZALE.” Luka 14:23. Kulira kwa Mulungu ndi kwakuti dziko lonse lipulumutsidwe, ndi kuti nyumba Yake-tchalitchi-lidzale! Kuchokera ku vumbulutso limeneri bukhu iri linabwera., “Mpingo Waukulu” lolembedwa ndi Bishop Dag Heward-Mills, m’busa wa umodzi mwa mipingo yaikulu kwambiri ku Ghana. Mpingo wanu ndi utumiki wanu sudzakhalanso chimodzi modzi mukawerenga bukhu lolimbikitsali!“Dr. Heward-Mills ndi wodzipereka kwa Ambuye Yesu Khristu ndi ntchito yotenga mbali pa kulalikira ku dziko lonse. Ndi mtsogoleri wamphamvu ndinso chitsanzo ku mautumiki onse, ndipo ife ku “Church Growth International”, ndife olemekezedwa kudziwa ndikumutcha Dr. Dag Heward-Mills mnzathu komanso wogwira naye limodzi ntchito mu kholola lalikulu mu minda ya padziko.” -Dr. Yonggi Cho Wamkulu, Church Growth International
  • Kodi mukudziwa kuti moyo wa munthu padziko lapansi ndi nkhondo? Tili pankhondo kaya tasankha kukhala pankhondo kapena ayi. Baibulo limati moyo wanu ndi nkhondo. Inu muyenera kumenya nkhondo yabwino ndi kupambana nkhondoyo. Bukhu latsopanoli pa nkhondo ndiloyenera kuwerengedwa ndi atsogoleri.
  • Kudzikweza ndi poizoni wakupha amene waononga mtundu wa anthu mzaka zambiri. Chifukwa nkosatheka, kudzikweza kumakwaniritsa kupangitsa chionongeko chachikulu popanda kuonekera. Tingamenyane bwanji ndi chiopsezo chimenechi ku miyoyo yathu? Ndi katemera wa kudzichepetsa! Kudzichepetsa ndi chabwino chauzimu. Ochepa akwanitsa kulemba zokhudzana ndi chofunikira chauzimuchi. Mu bukhu latsopano losangalatsali, Dag Heward-Mills akuonetsera mitundi yobisika ya kudzikweza. Bukhu la mphamvu limeneri, lolembedwa ndi Mkhristu wovutika mzathu, likudalitsani ndi kukulimbikitsani inu kukuza kudzichepetsa konga mwana kwa Yesu Khristu.
  • Yesu Khristu akuonetsera mfundo yodabwitsa yomwe ikutsogolera kuchita bwino ndi chuma. Iye amene ali nako kanthu azakhala nazo zambiri! Zikumveka mokondera! Koma, ichi ndi chilungamo chomwe chikuonetsedwa kwa ife tsiku ndi tsiku. Bukhuli likulongosola Lemba losamvetsetseka kwambiri iri. Muzalandira chidziwitso chachikulu ku zinsinsi za kuchita bwino pamene mukuwerenga bukhu latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Ngati ndinu m’busa wa nkhosa za Mulungu, muzathandizika kwambiri ndi ntchito yabwinoyi. Masamba amenewa ali ndi malangizo ofotokozedwa bwino, ofunikira pa kuchita bwino kwanu. Bishop Dag Heward-Mills akutenga kuchokera mukukhala kwake kwa zaka zoposera makumi atatu ngati m’busa, kugawana nafe zinthu zochita mu ntchio ya utumiki. Ngati mwasirira kukhala m’busa wa anthu a Mulungu, iri ndi bukhu lokutsogolerani lomwe mwakhala mukulifuna.
  • Tikudziwa kui kukula kwa mpingo ndi chinthu chovuta kukwaniritsa. azibusa onse amafuna mpingo wawo ukule. bukhuli ndi yankho la kufuna kwanu kwa kukula kwa mpingo. mukamvetsetsa momwe "zinthu zosiyanasiyana zimawirira pamodzi" kukwaniritsa kukula kwa mpingo. wokondedwa m'busa, pomwe mawu ndi kudzoza kuli m'bukhuli kukubwera mu mtima mwanu, muzakhala ndi kukula kwa mpingo komwe mwakhala mukupempherera.
  • Mawu a Chigiriki akuti LAIKOS akutanthauza “kupanda luso”. Mbiri yatiphunzitsa kwa nthawi ndi nthawi kuti zinthu zazikulu zakwaniritsidwa kudzera kwa anthu amene “anasowekera luso”. Phunzirani, kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, zomwe zimachitika pamene palibe anthu a wamba kugwira ntchito mu tchalitchi; momwe mungagawanirane zolemetsa ndi anthu wamba ndi momwe tikuyenera kulimbanira kuteteza utumiki wa wamba.

Title

Go to Top