• Iri ndi bukhu lolandiridwadi. Bishopu Dag Heward-Mills, m’busa iye mwini, akulongosola zifukwa ndi momwe ungapangire utumiki waubusa kuchita bwino.
  • Kubzala mipingo ndi chinthu chomwe chafalikira pakati pa azitumiki a uthenga wabwino. Inali ntchito ya ophunzira oyambirira. Kubzala mipingo kopambana kumafuna luso ndi zina zambiri. Dag Heward-Mills, woyambitsa matchalitchi zikwi zitatu padziko lonse, akutitsogolera ife kuunikira zinthu zosiyana siyana za kubzala mpingo mu bukhuli. Ili ndi kope la kuphunzirirapo kwa mtumiki ali yense amene akufuna kupanga kubzala mipingo kukhala masomphenya ake a moyo ndi utumiki.
  • Mau opatsa chidwi amenewa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi" analankhulidwa ndi Yesu Khristu pa gulu lake laling’ono la ophunzira khumi ndi awiri. Ambiri a ife timachitiridwa zowawa ndi mdierekezi chifukwa sitimadziwa momwe tingamuonetsera poyera kapenanso kukazindikira zintchito zake. Mu bukhu lodalitsika limeneli, mudzatulukira uchimo wa mdierekezi ndi kupanga chisankho cha kusayenda mmenemo. Zikhale kuti mau awa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi” asakhale akunenera pa inu!
  • Ngakhale ndi mutu wachilendo, kubwerera m’mbuyo kumachitirana ndi zopezeka mwa wamba mwa Akhristu. Ambiri amayamba, koma si ambiri amene amapirira. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward Mils akuchenjeza, ndi kuwonetsa zifukwa zomwe Mkhristu aliyense akuyenera kukafikira Kumwamba!
  • Kudzoza ndi chifungulo chachichikulu chofunikira kutsegula khomo la kuchita bwino ndo kukwaniritsa utumiki. Anthu ambiri ayesera kuchita ntchito ya Mulungu chifukwa cha mafuno abwino, popanda kufika kutali analephera kuzindikira kuti “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu Wanga (Kudzoza)” [Zekariya 4:4]. Bukhu lapderali “Kupeza Kudzoza” lolembedwa ndi Bishopu Dag Heward-mills lizakuphunzitsani inu zomwe zimatanthauza kupeza kudzoza ndi momwe mungapangire! Lolani chikhumbo khumbo cha Kudzoza kwa Mulungu kutakasike mkati mwanu kudzera mu masamba a m’bukhuli!
  • Bukhu iri ndi mphatso ina kuchokera ku cholembera cha Dag Heward-Mills kwa azitumiki onse amene atha kupeza nthawi yowerenga. Bukhuli lizayankha mafunso onse okhuzana ndi momwe mungakwaniritsire kukhala ndi ubale wabwino pakati pa atate ndi ana. Kudzera mu chiphunzitso cha bukhu limeneri, muzapewa themberero pa moyo wanu ndi kubweretsa kwanokha mdalitso. Atate ndi anthu apadera amene amakuza ana. Popanda atate sipazakhala ana kupitiriza utumiki ku mibadwo ina. Maitanidwe a Mulungu amakula kapena kufa ndi kuthekera kochitirana ndi atate. Werengani bukhu limeneri ndipo pewani themberero lokhuzana ndi kusalemekeza, kusamvera ndi kukhala ndi ubale woipa ndi atate.
  • Anthu amene amakusiya atha kukuwonongani. Palibe chimene chingalongosera kumva kwa kukhumudwa, kubalalika ndi nkhawa zimene zimadza pamene anthu akukusiyani. Bukhu ili lalembedwa kukuthandizani inu kulimbana ndi chiwonongeko chomwe chimadza pamene anthu akusiyani. Musanyengedwe. Kusiidwa sikwachilendo kwa inu ndi utumiki wanu. Ambiri ena avutika ndi zomwezo. Satana anali wopanduka woyamba ndipo akulimbikitsa opandukira onse kuyambira pamenepo. Ndi bukhu limeneri mu manja anu, muzachirimika ndi kulimbana ndi mzimu wa kusakhulupirika umene umadza ndi “iwo amene amakusiyani”.
  • Nthawi zambiri timalimbikitsika pamene tikamaganizira za mfundo yoti “Ambiri Aitanidwa”. Kenako tonse mwachangu timalimbikitsika tikamalingalira za mfundo yoti “…ochepa amasankhidwa.” Mutha kuwerengedwa ndi ambiri amene aitanidwa ndi ochepa amene asankhidwa ngati mupange bukhuli kukhala gawo la moyo wanu.Mu bukhu lodabwitsali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, muzazindikira kuchokera mu Baibulo zifukwa zomwe munganenere motsimikiza kuti ndinu oitanidwa. Inu mudzadziwa za makhalidwe a anthu oitanidwa ndipo muzalimbikitsidwa kukhala wosatekeseka mpaka kumapeto kwa ulendo wanu wa Chikhristu.
  • “Mwina mmodzi mwa adani aakulu omwe mutha kukumana nawo ndi ‘woneneza pakati pa abale’.” Landirani chidziwitso chachikulu cha momwe chida chimenechi cha kuneneza chimadzera ndipo phunzirani za momwe mungachigonjetsere, pomwe mukuwerenga bukhu lapamwambali, lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Baibulo limatilangiza ife ku: "Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzakeyo" (Afilipi 2:4). M'bukhu la m'nthawi yakeli, Dag Heward-Mills akukuwuzani inu mupitirire kuganiza za inu nokha ndi kuganizanso za ena! Mukondenso ena! Muganizirenso ena! Musamalenso za ena! Mukhalenso chifukwa cha ena! Yesu anadza kudzatifera ife chifukwa Iye anaganiza za "ena". Ine ndikufuna kukhala kwambiri ngati Iye. Kodi inu mukufuna kukhala ngati Yesu?
  • “Ndingapemphere bwanji? Kodi ndipempherere chani? Kodi pemphero ndilodabwitsa chifukwa chani? Ndingapemphere bwanji kwa nthawi yaitali? Kodi Mulungu sakudziwa zomwe ndikufuna? Mapemphero anga ayankhidwadi?” Pezani mayankho a mafunso amenewa pomwe mukuwerenga bukhu lobwera panthawi yake lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Mu bukhu lapamwambali, Bishop Dag Heward-mills amaphunzitsa za momwe chida cha kukhulupirika chimalimbikitsa kachitidwe ka mtsogoleri. Kugwiritsa ntchito baibulo, mbiri ndi zolemba, mutu uwu wapangidwa kukhala woyenera kwa wowerenga.

Title

Go to Top