-
Kodi mukudziwa kuti aneneri akale, anafunsa ndi kufufuza zachipulumutso chachikuluchi chomwe chawonetseredwa kwa ife? Iwo sakanaganiza za momwe chipulumutsochi chingabwerere kwa anthu…koma ndife odalitsika kulandira chipulumutsochi! Ife talandira chipulumutso chifukwa winawake adatiuza za ichi. M'bukhu lopatsa chidwili, Mlaliki Dag Heward-Mills akutitsogolera ife kuti tisangomvetsetsa chipulumutso chathu chachikulu komanso mmene tingagawire ena uthenga wabwino wa chipulumutso chachikuluchi. Aliyense mwaife akachite ntchito ya mlaliki!
-
Bukhuli ndi chiongolero chapadera ku kumvetsetsa chipulumutso kudzera mwa Yesu Khristu. Mu bukhu la pamwambali, muzamvetsetsa momwe Yesu amakukonderani inu, momwe mungabadwire mwatsopano, momwe mungapewere kupita ku gehena ndi chomwe chimatanthauza kukhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu. Perekani bukhuli kwa wina aliyense ndipo azamvetsetsa zomwe zikutanthauza kupulumutsidwa kudzera mu mwazi wa Yesu Khristu.
-
Mutu wa bukhuli likukupangitsani kuganiza pompopompo za ana ang'ono akuyimba mokondwa…Mumawerenga Baibulo lanu tsiku lililonse? Mumapemphera tsiku lililonse?Bukhu ili litsekula maso anu ku bukhu lodabwitsa lapalokha lotchedwa Baibulo. Likutsekuliraninso zozizwa zomwe zimadza kwa inu tsiku lililonse pamene mukuwerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku lililonse. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera kwanu kwa tsiku lililonse kukhale kosangalasa kwa inu!
-
Anthu ambiri amavutika ndi lingaliro la kupereka chakhumi ingakhale mchitidwe wakale kalewu wabweretsa chuma kwa Ayuda. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward-Mills akuphunzitsa momwe kupereka chakhumi kumapezera mfundo zikulu zikulu za kupanga chuma ndi zozwizitsa za kuchita bwino. Sangalalani ndi limodzi mwa makope a Dag Heward-Mills.
-
Dr. Dag Heward-Mills, mtsogoleri wa Chikhristu wopambana, akuonetsa chimodzi mwa zinsinsi zake. “Ngati wina atandifunsa chomwe chinsinsi changa chachikulu cha ubale wanga ndi Mulungu chiri, nditha kunena, musaopa, kuti ndi mphamvu ya nthawi za chete yomwe ndimakhala nayo ndi Iye tsiku ndi tsiku.” Iwe waganiza kulemba bukhuli kuti inunso mukapindule kuchokera ku mphamvu ya nthawi ya chete.
-
Baibulo limatiuza kuti tonse timalakwitsa- Abusa nawo amalakwitsanso. Kulakwitsa kumabwezeretsa m’mbuyo. Kulakwitsa kumalepheretsa kupita chitsogolo. Kodi ndi zolakwitsa ziti zimene abusa anu apanga? Kodi ndi chiyani chingakhale zolakwitsa zazikulu khumi zimene abusa amachita? Muli omasuka kuwerenga Bukuli ndi kuzindikira zolakwika zimene mungazichite ndi m'mene mungazipewere. Buku lofunikali lidzakhala mdalitso kwa inu ndi utumiki wanu.
-
Mu bukhu lapamwambali, Dag Heward-Mills akupereka kuzindikira kwakukulu kwa zochitika m'banja. Bukhu lodabwitsali likagwira ntchito ngati chipangizo chokonzekera kwa phungu wa banja ndi anthu okwatira. Inu mukapeza mu bukhuli, mfundo zotsitsimutsa ndi zosangalatsa zopititsa patsogolo banja lanu. "Bukhu ili ndilodzadza ndi nkhani pa maziko ndi zochitika pa maubwenzi a umunthu mu nthawi imene musanakwatire, muli m'banja ndi ngakhale utatha ukwati. Ili ndi zipangizo zofufuzidwa bwino ndi zovomerezeka pa thunthu ndi kakhalidwe kazolengedwa pazogonana, kubereka kwa anthu, mimba ndi nthawi yobereka ikadutsa. Kuthekera kwa Dotolo Dag Heward-Mills kusintha nkhani zovuta kukhala zophweka ndiye chikhalidwe chosiyanitsa pa bukhuli. Zonse pamodzi, izi zimalipangitsa kukhala bukhu losindikizika lomveka kwambiri, logwiritsika ntchito bwino pa zabanja lero." David Asomani, katswiri wowona za chiberekero cha azimayi. "Bukhu la Bishopu Dag Heward-Mills pa uphungu wa m'banja ndilosowa chifanizo. Maziko ake ngati dotolo wa zachipatala zawonetsedwa momveka bwino mu tsatanetsatane, koma kudzifotokozera kwa zizindikiro zachipatala zomwe zikupangitsa bukhuli kukhala lapadera." Edwin Morgan Ogoe, Mphunzitsi, Sukulu Yaukachenjede ya Ghana, Sukulu Yazachipatala
-
Perëndia ka thirrur shumë njerëz me të vërtetë. Jeta jonë në tokë është një mundësi për t’i shërbyer Atij dhe Perëndia vështron gjërat që po bëni për Mbretërinë e tij. Ky libër përbën një lexim stimulues. Nëse i përvetësoni të vërtetat e përçuara nga autori, do të merrni urtësi për të përdorur mundësitë e jetës suaj në mënyrën e duhur.