-
Tonse timalindirira moyo waulemerero komwe kuzakhala "KULIBENSO THEMBERERO!" Ichi ndi chifukwa choti mmoyo timakumana ndi matsoka, kuzunzika kopitirira, utsiru, kusasangalala ndi kukhumudwa. Themberero limafotokoza bwino matsoka okumana nawowa omwe tikuwoneka kuti timakumana nawo. Tingazipewe? Pali njira yosakumanirana nazo? Bukhuli likakuthandizani inu kumvetsetsa matemberero ndi momwe mungazikhadzikitsire nokha kuti mukalandire mdalitso. -
Bukhuli ndi chiongolero chapadera ku kumvetsetsa chipulumutso kudzera mwa Yesu Khristu. Mu bukhu la pamwambali, muzamvetsetsa momwe Yesu amakukonderani inu, momwe mungabadwire mwatsopano, momwe mungapewere kupita ku gehena ndi chomwe chimatanthauza kukhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu. Perekani bukhuli kwa wina aliyense ndipo azamvetsetsa zomwe zikutanthauza kupulumutsidwa kudzera mu mwazi wa Yesu Khristu. -
Baibulo limayankhula za mitundu yambiri ya mwazi: mwazi wa mbuzi, mwazi wa nkhosa, mwazi wa nkhunda! Baibulo limatiuzanso kuti popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo. Ndiye kodi umodzi mwa mitundu iyi ungather kuchotsa machimo?yankho ndi ‘Ayi’ wotsindika. Ndiye ndi chani chingachotse machimo athu? Palibe, koma mwazi wa Yesu Khristu! Ndi mwazi wa Yesu wokhawo umene uli ndi mphamvu kukachotsa machimo athu ndi kutibweretsera chipulumutso. Mu bukhu lofunikira kwambiri limeri, muzapeza zilungamo zoyera kwambiri zokhuzana ndi mwazi wa Yesu Khristu. Mupeza momwe mwazi wa Yesu umaperekera moyo ndi momwe mwazi wa Yesu unapezera kufunikira kwake. Muzamvetsetsa chiyanjano cha pakati pa Mzimu Woyera ndi mwazi wa Yesu. Mulidi mphamvu mu mwazi wa Yesu! -
Ku 1 Akorinto 12:28, Baibulo limatiuza za mphatso zingapo zimene Mulungu wapereka mu mpingo. Mphatso zosiyanasiyana izi pamodzi, zimathandiza mpingo wa Mulungu kuti upite patsogolo ndi mphamvu. Mphatso ya ulamuliro ndi imodzi mwa mphatso zimene Mulungu waika mu mpingo. Kodi utsogoleri wa mpingo uyenera kuyendetsedwa bwanji? Kodi atsogoleri ampingo ayenera kuchita chiyani? Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere: pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; Tiyenera kutenga mphatso ya utsogoleri mozama, ndipo bukhu lamtengo wapatali ili lolembedwa ndi Dag Heward-Mills lithandiza utsogoleri wa mpingo wanu, kayendetsedwe ka mipingo ndi ulamuliro wa mpingo munjira ya tsiku ndi tsiku! -
…ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro. Mateyu 24:14 Ndi chiyani chomwe chingathetse moyo monga mukudziwira? Kodi ndi mphamvu yanji yopangitsa kutha kwa zinthu zonse m'moyo wanu? Kodi chizindikiro cha kutha kwa utumiki wanu padziko lapansi chidzakhala chiyani? Kodi n’chiyani chidzathetse mpingo? Mapeto a chilichonse ndi imfa! Anthu ambiri otchulidwa m’bukhuli anatha momvetsa chisoni. Ndikofunika kudziwa chifukwa chomwe moyo wawo unathera. Ndikofunika kudziwa chifukwa chomwe mautumiki a anthu amathera. Kupyolera mu bukhu lounikirali, mudzaona kuti kudzikuza, kusamvera, chidani, kupotoza, kupanduka ndi kunyoza ndi zina mwa zinthu zosasangalatsa zimene zingawononge moyo wanu ndi utumiki wanu. Utumiki wanu uwomboledwe mathero a m’njira yatsoka mofananamo pamene mulandira nzeru zazikulu kuchokera m’bukhu losonkhezera maganizo limeneli. -
“…Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe. KUTI NYUMBA YANGA IDZALE.” Luka 14:23. Kulira kwa Mulungu ndi kwakuti dziko lonse lipulumutsidwe, ndi kuti nyumba Yake-tchalitchi-lidzale! Kuchokera ku vumbulutso limeneri bukhu iri linabwera., “Mpingo Waukulu” lolembedwa ndi Bishop Dag Heward-Mills, m’busa wa umodzi mwa mipingo yaikulu kwambiri ku Ghana. Mpingo wanu ndi utumiki wanu sudzakhalanso chimodzi modzi mukawerenga bukhu lolimbikitsali!“Dr. Heward-Mills ndi wodzipereka kwa Ambuye Yesu Khristu ndi ntchito yotenga mbali pa kulalikira ku dziko lonse. Ndi mtsogoleri wamphamvu ndinso chitsanzo ku mautumiki onse, ndipo ife ku “Church Growth International”, ndife olemekezedwa kudziwa ndikumutcha Dr. Dag Heward-Mills mnzathu komanso wogwira naye limodzi ntchito mu kholola lalikulu mu minda ya padziko.” -Dr. Yonggi Cho Wamkulu, Church Growth International -
Mulungu ali ndi dongosolo lalikulu lokuchulukitsa anthu ake ndi kuwawonjezera ngati gulu la nkhosa. Dongosolo la Mulungu ndilakuti anthu ake asakhale ochepa, ndipo asakhale ang’onoang’ono! Ili ndilo dongosolo la Mulungu pa inu. Kodi mwadzifunsapo ngati kukula kwa mpingo n’kotheka? Kodi mwalimbapo kuyesa njira zambiri zimene sizinagwire ntchito? Ili ndi bukulo limene munali mukulidikira! Landirani mawu aliwonse a ulosi olembedwa m’bukuli ndipo khulupirirani kuti akugwirizana ndi moyo wanu ndi utumiki wanu! Ndi mutu wina wofunika kwambiri mu mndandanda wa mabuku anu a “Kukula kwa Mpingo”; bukuli lidzakweza utumiki wanu kufika pamlingo wa mpingo wokula kawiri, mpingo wa utumwi waukulu kwambiri, kudzera mu njira zoyesedwa ndi kutsimikiziridwa zimene wolemba mwiniwake wagwiritsa ntchito, zokhala ndi zotsatira zosatsutsika! -
Anthu ambiri samamvetsetsa za malo a mtengo wa dzindikila chabwino ndi choipa m`moyo mwathu. Nthawi zambiri timaganiza kuti unali mtengo qmwe unalipo kalekale munthawi ya Adamu ndi Eva. Timakhulupirira kuti mtengo umeneyo unali ndi zipatso za poizoni zoti ukangodya yemwe wadyayo amafa. Mwa tsoka, Adamu ndi Eva anadya za mtengowu ndipo anafa. Tikawerenga za nkhaniyi, timaganiza kwa ife, “zinali zomvetsa chisoni Adam ndi Eva kudya chipatso chakuphachi koma tithokoze sitidzaikidwa m`mayeselo ndi mtengo ngati umenewo”. Zachisoni, tikhala tikulimbana ndi mtengo umenewu ndi zipatso zake. Chomwe tiyenera kudziwa ndi chakuti za mtengo wa kudzindikira chabwino ndi choipa udakalipobe mpaka lero. Umagwira ntchito m`mayesero kwa ife chimodzimodzi m`mene unapangira nthawi ya Adamu ndi Eva. Umayimilira ngati njira ina ya kwa Mulungu. -
Mau opatsa chidwi amenewa mwa inu mmodzi ndi mdierekezi" analankhulidwa ndi Yesu Khristu pa gulu lake lalingono la ophunzira khumi ndi awiri. Ambiri a ife timachitiridwa zowawa ndi mdierekezi chifukwa sitimadziwa momwe tingamuonetsera poyera kapenanso kukazindikira zintchito zake. Mu bukhu lodalitsika limeneli, mudzatulukira uchimo wa mdierekezi ndi kupanga chisankho cha kusayenda mmenemo. Zikhale kuti mau awa mwa inu mmodzi ndi mdierekezi asakhale akunenera pa inu! -
Mu buku lopambanali, Dag Heward-Mills akusanthula zinthu zochitikadi mu utumiki masiku ano. Akukamba za zinthu zochitika zokhudza zachuma, ndale, kucheza ndi amuna kapena akazi komanso maubale mu utumiki. Bukuli ndi muuni wa makhalidwe otsatira mwambo pa mayitanidwe anu ndipo ndi buku lomwe mtsogoleri wachikhristu aliyense akuyenera kukhala nalo. Ndi lovomerezeka ku sukulu za Baibulo ndi kwa atumiki onse. -
Bukhuli lizachiza kusweka mitima kwa ana aakazi! Mubukhu loyembekezerekali, akazi akulimbikitsika kulola nzeru ya Mulungu kuwathandiza iwo kugonjetsa zinthu zosatheka zambiri zomwe amakumana nazo. Mulungu adzakhuza moyo wanu ndi kulimbikitsa inu pamene mukulimva bwino bukhu lamphamvu latsopanoli maka maka kwa ana aakazi. -
Utumiki wa Yesu Khristu si katundu wolemetsa. Ndi mwayi wapadera! Mwayi wapadera ndi ufulu kapena phindu limene limapatsidwa kwa anthu ena osati kwa ena onse. Mwayi wapadera ndi mwayi wapadera wochita chinachake. Mwayi wapadera ndi phindu lapadera limene si aliyense amene amasangalala nalo. Mwayi wapadera ndi phindu limene limasangalalidwa ndi anthu ena okhaokha. Mwayi wapadera ndi kuchotsedwa pa malamulo ena kapena kupatsidwa chiloledwe chapadera, chomwe chimaperekedwa kwa anthu ena okhaokha. Kutumikira anthu a Mulungu kudzakhala nthawi zonse mwayi wapadera. Palibe ulemu waukulu komanso palibe mwayi waukulu kuposa kukhala mtumiki wa Mulungu Wam’mwambamwamba! Pamene Mulungu anakuyitanani kuti mukhale m’busa, ankakupatsani mwayi wapadera umene anthu ambiri sazaupeza. Dziwani zambiri za mwayi wapaderawu wokhala mtumiki wa Mulungu kudzera m’bukuli lodzutsa mtima lolembedwa ndi Bishop Dag Heward-Mills, wolemba mndandanda wogulitsa kwambiri wa mabuku a Loyalty and Disloyalty.