-
Mutha kukhala kuti munamvapo kuti ndi chinthu chachikulu kutumikira Ambuye; koma inu mutha kukhala kuti simunaganizire bwino momwe chili chabwino zedi kutumikira Ambuye Mulungu wathu. M'bukhu lapaderali la Dag Heward-Mills inu mukamvetsa kuti mtumiki wa Mulungu ndindani ndi momwe inu mungamutumikirire Ambuye. Mukadziwe mochita kusiyana pakati pa iwo amene amamutumikira Ambuye ndi iwo amene samutumikira Iye! Inu mukawerengedwe ndi iwo amene amamutumikira Ambuye! -
Padziko lonse lapansi, ana amaphunzitsidwa kunena “Zikomo.” Makafukufuku akusonyeza kuti kunena “Zikomo” timaphunzitsidwa kuyambira tili ana aang’ono kwambiri. Komabe, Baibulo limanena kuti m’masiku otsiriza anthu adzakhala osayamika! Buku labwino kwambiri ili, lolembedwa ndi wolemba wotchuka Dag Heward‑Mills, limatiphunzitsa momwe tingapitirire kukhala oyamikira, ndipo limafotokoza zimene zimachitikira amene samayamikira. Udzadalitsidwa ndipo udzalimbikitsidwa kukhala m’gulu la oyamikira pamene ukamatembenuza masamba odzozedwa awa -
Akhristu ambiri sadziwa kufunikira kwa Chihema cha Msonkhano m’kuyenda kwawo kwa tsiku ndi tsiku ndi Mulungu. Ambiri a ife sitikumvetsa mbali zosiyanasiyana za Chihema cha Msonkhano. Ndithudi, ambiri a ife timadabwa ndi tsatanetsatane wapadera umene Mulungu anapereka pa kumanga Chihema cha Msonkhanochi. Chihema cha Msonkhano chinali malo omangidwa mosamala kwambiri, achinsinsi, a kupezeka kwa Mulungu. M’chiphunzitso chakuya chimenechi, timayenda kudzera mu Chihema cha Mulungu. Zisindikizo zatsegulidwa kuti zitithandize kumvetsa Chihema cha Mulungu ndi kupezeka kwa Mulungu pakati pa anthu. -
Kodi Mumakonda Ambuye? Limeneli ndi funso lofunikira! Ambuye wathu, Yesu Khristu, anafunsa Petro, "Petro umandikonda Ine?" Chifukwa chiyani chikondi chanu pa Mulungu ndi chinthu chimene tiyenera kukambilana? Yesu akuti lamulo lalikulu ndilakuti "mumukonde Ambuye Mulungu wako, ndi Mtima wako wonse, moyo wako wonse ndi malingaliro ako onse." Nthawi zina, pamakhala nyengo zina zimayikidwa pamodzi komanso kuperekedwa kwa inu ndi Ambuye zimene zili mayesero, mayesero otsimimizira umboni wanu pa Ambuye. Ngati mumakonda Ambuye, tsimikizirani pa kupambana mayesero a chikondi! Bukhu lina lodabwitsa la mlembi wotchuka, Dag Heward-Mills, limene likupangitseni kuganiza komanso kudzifunsa nokha funso lofunikira lonse "Kodi ndimakondadi Ambuye?" -
Pachiyambi panali Mawu! Mawu anali ndi Mulungu! Mawu anali Mulungu! Mulungu ndi Mawu Ake nthawi zonse amakhala pachimake ndi chiyambi cha chilichonse chaphindu. Kuti moyo wanu ukhale wa chinthu chilichonse, Mulungu ndi Mawu Ake ayenera kukhala chinthu chachikulu. Nzeru zanu zimasonyeza mmene mumaganizira. Nzeru zimakupangani kukhala munthu wothandiza. Munthu wanzeru amamanga kanthu. Zimene mwamanga zimasonyeza nzeru zanu. Nzeru ndiye chinsinsi chautsogoleri chomwe mungafune pautumiki. Nzeru ndiye chinsinsi chothana ndi zovuta za utsogoleri. Solomo anapempha nzeru kwa Mulungu. Mulungu anam’patsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu. Chotsatira cha mtima wanzeru ndi wozindikira umenewu chimawonekera m’Baibulo lonse. Bukhuli silinena za kuchenjera kwa anthu kapena zolankhula zonyenga. Bukhuli silikunena za mawu omveka bwino omwe amagwiritsidwa ntchito kusokoneza anthu. Mlembi, Bishopu Dag Heward-Mills, amafuna kuunikira owerenga kuti ngakhale pali mitundu yosiyanasiyana ya nzeru, mawu a Mulungu ndiwo apambana. -
Pali kusiyana kwakukulu pakati pa kulawa chinachake ndi kutenga nawo gawo. Kulawa chinachake ndiko kuchidya kapena kuchiyesa pa lilime; kutenga nawo gawo ndiko kupitirira kulawa ndi kuzidya. Kabukhu kakang’ono kochititsa chidwi kameneka, kolembedwa ndi Dag Heward-Mills, ndi kokamba za kutumikira Mulungu mopyola mlingo wa munthu wolawa. Mulungu akufuna kuti mutenge nawo zinthu zazikulu zimene wapereka kwa inu mu utumiki. Palibe chifukwa chokhalira olawa pamene mungakhale otenga nawo gawo mu zinthu za Mulungu! -
Wophunzira ndi watsopano ku chinachake; iye ndi woyamba. Mulungu si munthu amene wangoikidwa kumene kapena wolengedwa kumene. Palibe chilichonse chokhudza Mulungu chomwe chimamupanga kukhala watsopano. Iye ndiye chiyambi! Mulungu wakhala alipo kuyambira kalekale. Iye ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova wamuyaya. Ndife omwe titha kukhala ongophunzira. Ndife amene timapeza zatsopano tsiku lililonse. Ongophunzira ndi wotseguka ku zoopsa zambiri monga kudzikuza. Ndi kudzikuza kwa munthu amene wangoyamba kumene kumamupangitsa kudzikweza yekha motsutsana ndi maulamuliro omwe akhazikitsidwa kwa zaka zambiri. Lusifara anali wophunzira amene anadzudzulidwa chifukwa cha kudzikuza kwake! Iye anagwa mu “chiweruzo cha mdierekezi”. Kulakwitsa kwakukulu kwa Lusifara kunali kuti analibe kudziyesa koyenera kwa iye mwini mogwirizana ndi Mulungu. Kupyolera m’mitu yochititsa chidwi imeneyi, mulole kuti mutenge ziphunzitso za kudzikuza kwa wophunzira mozama kwambiri, kuopera kuti mungakhale ndi moyo kuti mukwaniritse mfundo iliyonse ya m’bukhu lino kuti mudziwonongere nokha ndi kutsutsidwa. Pulumukani ku ngozi iliyonse ya wongophunzira! -
Moyo padziko lapansili umakhudzidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. Kodi mwakhalapo mukudabwa chifukwa chiyani moyo umadzaza ndi zotsatira zosayembekezereka ngakhale mutayika khama lonse kuti muchite bwino? Pali zinthu, zigawo, inde zokhazikitsa zimene zimakhudza zotsatira za zinthu zimene timachita. M'bukuli mudzakumana ndi zokhazikitsa zimene zimadutsa m'njira ya aliyense. Bukuli likukupatsani mwayi wopindula kwambiri pa mpikisano wa moyo! Mutsogoleredwe ndi chivumbulutso cha bukuli, kuti muyende monga munthu wodziwa kuti "nthawi ndi mwayi zimachitikira tonsefe." Lolani zokhazikitsa zimenezi zikankhire moyo wanu patsogolo!