-
Mutu wa bukhuli likukupangitsani kuganiza pompopompo za ana ang'ono akuyimba mokondwa…Mumawerenga Baibulo lanu tsiku lililonse? Mumapemphera tsiku lililonse?Bukhu ili litsekula maso anu ku bukhu lodabwitsa lapalokha lotchedwa Baibulo. Likutsekuliraninso zozizwa zomwe zimadza kwa inu tsiku lililonse pamene mukuwerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku lililonse. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera kwanu kwa tsiku lililonse kukhale kosangalasa kwa inu! -
Anthu ambiri amaganiza kuti zaka zawo zaunyamata ziyenera kuthera popanga zopusa ndi kuchita masewera. Iwo amaganiza kuti zinthu za Mulungu ndi za anthu okalamba, osaganiza bwino, okhwima maganizo, odziwa zambiri amene akhalapo m’dzikoli ndipo akumana ndi mavuto ambiri. Dag Heward-Mills ndi ngwazi ya achinyamata. Iye amakhulupirira kwambiri kuti achinyamata ndi okhoza kwambiri kutumikira Mulungu ndi kumutumikira m’njira yopambana kwambiri. Buku lopatsa chidwi komanso lophunzitsa modabwitsali, likupatsani zinthu zambiri zomwe muyenera kukhala Okonzeka pa zaka 20 kuchita! Kodi muli ndi zaka makumi awiri kapena kuposerapo? Ndiye mwakonzeka kulowa nawo gulu lankhondo la Ambuye. -
Mzimu Woyera amafotokozedwa m’njira zambiri: monga mtsinje, monga madzi, monga mphepo, monga mafuta, monga blanketi, monga nkhunda, ndi zina zotero. Kuyenda mu kudzodzedwa ndi kuyenda limodzi ndi Mzimu Woyera m’njira zosiyanasiyana zimene Iyeyo amadzionetsera yekha. Zikuchitikireni kuti muzipeza Mzimu Woyera mkati mwanu, pamodzi nanu komanso pa inu! Ndikupemphera kuti muzilola dzanja lamphamvu la Mulungu likutsogolereni pamene mukungoyenda naye momasuka! -
Bola Mulungu akutipatsa moyo, tili ndi mwayi wochita zinthu zazikulu. Lero uli ndi mwayi woyesa kuchita zinthu zazikulu za Mulungu. Osachepera, yesa! Panga kuyesa! Ili ndi buku lomwe lidzakulimbikitsa kuti ukhale wabwino kwambiri, mmene Mulungu anakupangira kuti ukhale. Dzipatse chiganizo choyesa kuchita zinthu zazikulu za Mulungu tsiku lililonse, ndipo udzadabwa ndi zimene udzatha kuchita mwa chisomo cha Mulungu. Zopambana zazikulu zikukudikirirani pamene umafufuza mosamala zomwe zili m’bukuli ndi kuyesa kuchita chinachake chachikulu chifukwa cha Mulungu! Muzachita zopambana za Mulungu! -
Phunziro losangalatsa komanso lozama ili pa mutu wa “chikhulupiriro” lidzakopa wina aliyense yemwe cholinga chake ndi kukondweretsa Mulungu. Pakuti popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu, malemba amanena choncho. Ichi ndichifukwa chake bukuli ndilofunika kuwerengedwa ndi aliyense amene ali ndi chikhumbo chokondweretsa Mulungu. Ngati chikhulupiriro chinapangitsa Abrahamu kukhala bwenzi la Mulungu, ndiye kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri pa kuyenda kwathu ndi Mulungu. Bukuli ndi chuma chenicheni! Dziwani zinsinsi zofunika kuti muyende ndi kukhala ndi moyo mwa chikhulupiriro. Tsegulani zinsinsi za chikhulupiriro zomwe mukuzifunikira kuti muchite zinthu zosatheka m’moyo wanu! -
Moyo ungakhale wovuta kwa aliyense. Nthawi zambiri chomwe mukufuna kuti mugonjetse chomwe inu mwagwamo ndi nzeru. Nzeru ndi chinsinsi cha Mulungu chomwe chikuthandizeni inu kuwuka kuchokera nkulimbana ndikukhala chozizwitsa chamoyo. Mulungu wakuikani inu ku ulemerero. Chinsinsi cha Mulungu ndi nzeru ya Mulungu mu chinsinsi chomwe chaikidwa pa ulemerero ndi kukongola kwanu. Zibvumbulutso za bukhuli zikubweretsereni chigonjetso tsiku lililonse! Bukhu ili likupatseni chidziwitso ndi kupambana! -
Lonjezo ili pa Yobu 8:7 : “Chingakhale chiyambi chako chinali chaching’ono, koma chimaliziro chako chidzachuluka ndithu” chikutisonyeza kuti Mulungu ali ndi cholinga cha kukula ndi kutukumuka kwa miyoyo yathu. Ndi dalitso lotani nanga kulowetsedwa m’zinsinsi zimene zidzatsogolera ku kukulitsa kwathu! Kupyolera mu zinsinsi zambiri zakukulitsa zovumbulutsidwa ndi wolemba, Dag Heward-Mills, tikuphunzira kuti kukulitsa kudzabwera kwa inu kupyolera mu zowawa, mndandanda wa nkhondo, kupambana ndi kulandira cholowa cha Mulungu. Tikuphunziranso kuti mutha kukulitsidwa mukamagwiritsa ntchito zinsinsi zakukulitsa za kusinkhasinkha, mbiri yakale, mabuku ndi nzeru. Kukulitsa kungathenso kubwera kwa inu kudzera mu nsembe ndi mphamvu zauzimu. Phunzirani zinsinsi zomwe zafotokozedwa m'bukhuli ndi kupindula ndi choonadi chake chodabwitsa. -
Kodi Chimachitika Ndi Chiyani Mukabadwa Mwatsopano? Mzimu wa Mulungu azabwera pa inu, komanso mumtima mwanu. Kenako mkati mwanu mudzabadwa kapena kupangidwanso. Mulungu amakupatsani mtima watsopano ndi mzimu zonse! Ndi mzimu wanu watsopano, mumakhala munthu watsopano kapena cholengedwa chatsopano. Mwakonzeka kukhala moyo watsopano. Moyo watsopanowu ndiwotheka chifukwa ndiwe munthu watsopano wamtima watsopano. Kubadwa mwatsopano ndikosavuta monga choncho. Anthu amafuna kuchita zinthu zovuta. Koma kubadwanso mwatsopano ndikosavuta! -
Baibulo limatiuza kuti tonse timalakwitsa- Abusa nawo amalakwitsanso. Kulakwitsa kumabwezeretsa m’mbuyo. Kulakwitsa kumalepheretsa kupita chitsogolo. Kodi ndi zolakwitsa ziti zimene abusa anu apanga? Kodi ndi chiyani chingakhale zolakwitsa zazikulu khumi zimene abusa amachita? Muli omasuka kuwerenga Bukuli ndi kuzindikira zolakwika zimene mungazichite ndi m'mene mungazipewere. Buku lofunikali lidzakhala mdalitso kwa inu ndi utumiki wanu.