• Chinthu chimodzi chokha chimadza kwa inu mukamva mawu akuti "M’busa" - nkhosa! Nkhosa ndi nyama zodalira zome zimafunikira abusa. M’busa ndi wotsogolera wosamalira komanso wachikondi kwa nkhosa. M'Baibulo, Mulungu amatitchula ife ngati gulu la nkhosa za Mulungu. Yesu adamuuza wophunzira Petro kuti adyetse nkhosa zake kuti atsimikizire za chikondi chake cha Mpulumutsi. Kukhala m'busa ndi ntchito yabwino kwambiri. Ndi chinthu chapamwamba kuitanidwa ndi Mulungu ndi kulembetsedwa mwa antchito Ake ndi kusamalira nkhosa. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutiitanira ife, akutilimbikitsa ndi kutiwonetsa ife momwe tingatengerepo nawo mbali pa ntchito yayikulu yosamalira anthu a Mulungu. Musati muzisiyidwe kunja kwa ntchito yabwino iyi yokhala m’busa!
  • Yesu anati: mukhale ochenjera ngati njoka ndi oona mtima ngati nkhunda. Kodi njoka ndizochenjeradi? Nchifukwa chiyani Yesu angapereke langizo ngati limeneli? Tengani kaulendo mu bukhu lopangitsa chidwiri la Dag Heward-Mills, ndi kuzipezera nzeru zobisika za njoka.
  • Baibulo ladzaza ndi mawu olimbikitsa kuti tizipemphera: "Zonse mu pemphero! Kukhala mukupemphera nthawi zonse! Anthu ayenera nthawi zonse kupemphera! Pempherani nthawi zonse! Pempherani osasiyasiya!" M'bukuli lodabwitsali, "Zonse mu pemphero, palibe popanda pemphero", mudzayamba ulendo wokuphunzitsani njira ndi makhalidwe a moyo wa pemphero wa Yesu Khristu. Ngati Yesu ankapemphera, ndiye kuti ine ndi iwe tiyenera kupemphera kwambiri. Chilichonse m'moyo mwathu chingakwaniritsidwe kudzera mu pemphero ndipo palibe chimene chingakwaniritsidwe popanda pemphero. Moyo wako wa pemphero udzakhala wosangalatsa kwambiri ukatha kuwerenga bukuli losangalatsa!
  • Mkhristu amayenda mkati kati mwa zoopsa zambiri ndi misampha. Bukhuli likatsekula maso anu ku zoopsa zambiri zobisika zomwe zikudikira kukupwetekani, kuvulaza komanso kuononga. Dzithandizeni nokha, dzipulumutseni nokha kudzera mu bukhu lamphamvu ili la zoopsa zauzimu!

Title

Go to Top