-
Bukhu iri ndi mphatso ina kuchokera ku cholembera cha Dag Heward-Mills kwa azitumiki onse amene atha kupeza nthawi yowerenga. Bukhuli lizayankha mafunso onse okhuzana ndi momwe mungakwaniritsire kukhala ndi ubale wabwino pakati pa atate ndi ana. Kudzera mu chiphunzitso cha bukhu limeneri, muzapewa themberero pa moyo wanu ndi kubweretsa kwanokha mdalitso. Atate ndi anthu apadera amene amakuza ana. Popanda atate sipazakhala ana kupitiriza utumiki ku mibadwo ina. Maitanidwe a Mulungu amakula kapena kufa ndi kuthekera kochitirana ndi atate. Werengani bukhu limeneri ndipo pewani themberero lokhuzana ndi kusalemekeza, kusamvera ndi kukhala ndi ubale woipa ndi atate.
-
Kudzoza ndi chifungulo chachichikulu chofunikira kutsegula khomo la kuchita bwino ndo kukwaniritsa utumiki. Anthu ambiri ayesera kuchita ntchito ya Mulungu chifukwa cha mafuno abwino, popanda kufika kutali analephera kuzindikira kuti “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu Wanga (Kudzoza)” [Zekariya 4:4]. Bukhu lapderali “Kupeza Kudzoza” lolembedwa ndi Bishopu Dag Heward-mills lizakuphunzitsani inu zomwe zimatanthauza kupeza kudzoza ndi momwe mungapangire! Lolani chikhumbo khumbo cha Kudzoza kwa Mulungu kutakasike mkati mwanu kudzera mu masamba a m’bukhuli!
-
Mau opatsa chidwi amenewa mwa inu mmodzi ndi mdierekezi" analankhulidwa ndi Yesu Khristu pa gulu lake lalingono la ophunzira khumi ndi awiri. Ambiri a ife timachitiridwa zowawa ndi mdierekezi chifukwa sitimadziwa momwe tingamuonetsera poyera kapenanso kukazindikira zintchito zake. Mu bukhu lodalitsika limeneli, mudzatulukira uchimo wa mdierekezi ndi kupanga chisankho cha kusayenda mmenemo. Zikhale kuti mau awa mwa inu mmodzi ndi mdierekezi asakhale akunenera pa inu!
-
Kubzala mipingo ndi chinthu chomwe chafalikira pakati pa azitumiki a uthenga wabwino. Inali ntchito ya ophunzira oyambirira. Kubzala mipingo kopambana kumafuna luso ndi zina zambiri. Dag Heward-Mills, woyambitsa matchalitchi zikwi zitatu padziko lonse, akutitsogolera ife kuunikira zinthu zosiyana siyana za kubzala mpingo mu bukhuli. Ili ndi kope la kuphunzirirapo kwa mtumiki ali yense amene akufuna kupanga kubzala mipingo kukhala masomphenya ake a moyo ndi utumiki.
-
Mawu a Chigiriki akuti LAIKOS akutanthauza “kupanda luso”. Mbiri yatiphunzitsa kwa nthawi ndi nthawi kuti zinthu zazikulu zakwaniritsidwa kudzera kwa anthu amene “anasowekera luso”. Phunzirani, kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, zomwe zimachitika pamene palibe anthu a wamba kugwira ntchito mu tchalitchi; momwe mungagawanirane zolemetsa ndi anthu wamba ndi momwe tikuyenera kulimbanira kuteteza utumiki wa wamba.
-
Tikudziwa kui kukula kwa mpingo ndi chinthu chovuta kukwaniritsa. azibusa onse amafuna mpingo wawo ukule. bukhuli ndi yankho la kufuna kwanu kwa kukula kwa mpingo. mukamvetsetsa momwe "zinthu zosiyanasiyana zimawirira pamodzi" kukwaniritsa kukula kwa mpingo. wokondedwa m'busa, pomwe mawu ndi kudzoza kuli m'bukhuli kukubwera mu mtima mwanu, muzakhala ndi kukula kwa mpingo komwe mwakhala mukupempherera.
-
Ngati ndinu m’busa wa nkhosa za Mulungu, muzathandizika kwambiri ndi ntchito yabwinoyi. Masamba amenewa ali ndi malangizo ofotokozedwa bwino, ofunikira pa kuchita bwino kwanu. Bishop Dag Heward-Mills akutenga kuchokera mukukhala kwake kwa zaka zoposera makumi atatu ngati m’busa, kugawana nafe zinthu zochita mu ntchio ya utumiki. Ngati mwasirira kukhala m’busa wa anthu a Mulungu, iri ndi bukhu lokutsogolerani lomwe mwakhala mukulifuna.
-
Yesu Khristu akuonetsera mfundo yodabwitsa yomwe ikutsogolera kuchita bwino ndi chuma. Iye amene ali nako kanthu azakhala nazo zambiri! Zikumveka mokondera! Koma, ichi ndi chilungamo chomwe chikuonetsedwa kwa ife tsiku ndi tsiku. Bukhuli likulongosola Lemba losamvetsetseka kwambiri iri. Muzalandira chidziwitso chachikulu ku zinsinsi za kuchita bwino pamene mukuwerenga bukhu latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
-
Kudzikweza ndi poizoni wakupha amene waononga mtundu wa anthu mzaka zambiri. Chifukwa nkosatheka, kudzikweza kumakwaniritsa kupangitsa chionongeko chachikulu popanda kuonekera. Tingamenyane bwanji ndi chiopsezo chimenechi ku miyoyo yathu? Ndi katemera wa kudzichepetsa! Kudzichepetsa ndi chabwino chauzimu. Ochepa akwanitsa kulemba zokhudzana ndi chofunikira chauzimuchi. Mu bukhu latsopano losangalatsali, Dag Heward-Mills akuonetsera mitundi yobisika ya kudzikweza. Bukhu la mphamvu limeneri, lolembedwa ndi Mkhristu wovutika mzathu, likudalitsani ndi kukulimbikitsani inu kukuza kudzichepetsa konga mwana kwa Yesu Khristu.