• Kudzoza ndi chifungulo chachichikulu chofunikira kutsegula khomo la kuchita bwino ndo kukwaniritsa utumiki. Anthu ambiri ayesera kuchita ntchito ya Mulungu chifukwa cha mafuno abwino, popanda kufika kutali analephera kuzindikira kuti “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu Wanga (Kudzoza)” [Zekariya 4:4]. Bukhu lapderali “Kupeza Kudzoza” lolembedwa ndi Bishopu Dag Heward-mills lizakuphunzitsani inu zomwe zimatanthauza kupeza kudzoza ndi momwe mungapangire! Lolani chikhumbo khumbo cha Kudzoza kwa Mulungu kutakasike mkati mwanu kudzera mu masamba a m’bukhuli!
  • Ngakhale ndi mutu wachilendo, kubwerera m’mbuyo kumachitirana ndi zopezeka mwa wamba mwa Akhristu. Ambiri amayamba, koma si ambiri amene amapirira. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward Mils akuchenjeza, ndi kuwonetsa zifukwa zomwe Mkhristu aliyense akuyenera kukafikira Kumwamba!
  • Mau opatsa chidwi amenewa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi" analankhulidwa ndi Yesu Khristu pa gulu lake laling’ono la ophunzira khumi ndi awiri. Ambiri a ife timachitiridwa zowawa ndi mdierekezi chifukwa sitimadziwa momwe tingamuonetsera poyera kapenanso kukazindikira zintchito zake. Mu bukhu lodalitsika limeneli, mudzatulukira uchimo wa mdierekezi ndi kupanga chisankho cha kusayenda mmenemo. Zikhale kuti mau awa “mwa inu mmodzi ndi mdierekezi” asakhale akunenera pa inu!
  • Kubzala mipingo ndi chinthu chomwe chafalikira pakati pa azitumiki a uthenga wabwino. Inali ntchito ya ophunzira oyambirira. Kubzala mipingo kopambana kumafuna luso ndi zina zambiri. Dag Heward-Mills, woyambitsa matchalitchi zikwi zitatu padziko lonse, akutitsogolera ife kuunikira zinthu zosiyana siyana za kubzala mpingo mu bukhuli. Ili ndi kope la kuphunzirirapo kwa mtumiki ali yense amene akufuna kupanga kubzala mipingo kukhala masomphenya ake a moyo ndi utumiki.
  • Iri ndi bukhu lolandiridwadi. Bishopu Dag Heward-Mills, m’busa iye mwini, akulongosola zifukwa ndi momwe ungapangire utumiki waubusa kuchita bwino.
  • Mawu a Chigiriki akuti LAIKOS akutanthauza “kupanda luso”. Mbiri yatiphunzitsa kwa nthawi ndi nthawi kuti zinthu zazikulu zakwaniritsidwa kudzera kwa anthu amene “anasowekera luso”. Phunzirani, kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, zomwe zimachitika pamene palibe anthu a wamba kugwira ntchito mu tchalitchi; momwe mungagawanirane zolemetsa ndi anthu wamba ndi momwe tikuyenera kulimbanira kuteteza utumiki wa wamba.
  • Tikudziwa kui kukula kwa mpingo ndi chinthu chovuta kukwaniritsa. azibusa onse amafuna mpingo wawo ukule. bukhuli ndi yankho la kufuna kwanu kwa kukula kwa mpingo. mukamvetsetsa momwe "zinthu zosiyanasiyana zimawirira pamodzi" kukwaniritsa kukula kwa mpingo. wokondedwa m'busa, pomwe mawu ndi kudzoza kuli m'bukhuli kukubwera mu mtima mwanu, muzakhala ndi kukula kwa mpingo komwe mwakhala mukupempherera.
  • Ngati ndinu m’busa wa nkhosa za Mulungu, muzathandizika kwambiri ndi ntchito yabwinoyi. Masamba amenewa ali ndi malangizo ofotokozedwa bwino, ofunikira pa kuchita bwino kwanu. Bishop Dag Heward-Mills akutenga kuchokera mukukhala kwake kwa zaka zoposera makumi atatu ngati m’busa, kugawana nafe zinthu zochita mu ntchio ya utumiki. Ngati mwasirira kukhala m’busa wa anthu a Mulungu, iri ndi bukhu lokutsogolerani lomwe mwakhala mukulifuna.
  • Yesu Khristu akuonetsera mfundo yodabwitsa yomwe ikutsogolera kuchita bwino ndi chuma. Iye amene ali nako kanthu azakhala nazo zambiri! Zikumveka mokondera! Koma, ichi ndi chilungamo chomwe chikuonetsedwa kwa ife tsiku ndi tsiku. Bukhuli likulongosola Lemba losamvetsetseka kwambiri iri. Muzalandira chidziwitso chachikulu ku zinsinsi za kuchita bwino pamene mukuwerenga bukhu latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Kudzikweza ndi poizoni wakupha amene waononga mtundu wa anthu mzaka zambiri. Chifukwa nkosatheka, kudzikweza kumakwaniritsa kupangitsa chionongeko chachikulu popanda kuonekera. Tingamenyane bwanji ndi chiopsezo chimenechi ku miyoyo yathu? Ndi katemera wa kudzichepetsa! Kudzichepetsa ndi chabwino chauzimu. Ochepa akwanitsa kulemba zokhudzana ndi chofunikira chauzimuchi. Mu bukhu latsopano losangalatsali, Dag Heward-Mills akuonetsera mitundi yobisika ya kudzikweza. Bukhu la mphamvu limeneri, lolembedwa ndi Mkhristu wovutika mzathu, likudalitsani ndi kukulimbikitsani inu kukuza kudzichepetsa konga mwana kwa Yesu Khristu.
  • Kodi mukudziwa kuti moyo wa munthu padziko lapansi ndi nkhondo? Tili pankhondo kaya tasankha kukhala pankhondo kapena ayi. Baibulo limati moyo wanu ndi nkhondo. Inu muyenera kumenya nkhondo yabwino ndi kupambana nkhondoyo. Bukhu latsopanoli pa nkhondo ndiloyenera kuwerengedwa ndi atsogoleri.
  • “…Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe. KUTI NYUMBA YANGA IDZALE.” Luka 14:23. Kulira kwa Mulungu ndi kwakuti dziko lonse lipulumutsidwe, ndi kuti nyumba Yake-tchalitchi-lidzale! Kuchokera ku vumbulutso limeneri bukhu iri linabwera., “Mpingo Waukulu” lolembedwa ndi Bishop Dag Heward-Mills, m’busa wa umodzi mwa mipingo yaikulu kwambiri ku Ghana. Mpingo wanu ndi utumiki wanu sudzakhalanso chimodzi modzi mukawerenga bukhu lolimbikitsali!“Dr. Heward-Mills ndi wodzipereka kwa Ambuye Yesu Khristu ndi ntchito yotenga mbali pa kulalikira ku dziko lonse. Ndi mtsogoleri wamphamvu ndinso chitsanzo ku mautumiki onse, ndipo ife ku “Church Growth International”, ndife olemekezedwa kudziwa ndikumutcha Dr. Dag Heward-Mills mnzathu komanso wogwira naye limodzi ntchito mu kholola lalikulu mu minda ya padziko.” -Dr. Yonggi Cho Wamkulu, Church Growth International

Title

Go to Top