Dag Heward-Mills ndi wolemba wa mabuku ambiri, kuphatikizapo logulitsidwa kwambiri “Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika”. Ndi woyambitsa wa Mipingo ingapo yochokera ku Lighthose ndi matchalitchi zikwi zitatu.
Dag Heward-Mills, mvangeli wadziko lonse, amatumikira mu misonkhano ya machiritso mu maiko komanso misonkhano ya atsogoleri padziko lonse. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa
www.daghewardmills.org.
-
Anagkazo amatanthauza “kukakamiza”.Amatanthauzanso kupangitsa kuti chifunike, kukusira, ndi kupanikiza mwa njira iliyonse monga kuumiriza, kuwopseza, kukopa ndi kuchonderera. Nthawi zina tiyenera kubwerera ku Chigiriki kuti timvetsetse matanthauzo enieni la mawu ena a M'baibulo. Mukuona, Chipangano Chatsopano chinamasuliridwa kuchokera kuchilankhulo cha Chigiriki ndipo Chipangano Chakale kuchokera ku Chihebri. Anagkazo ndi liwu la Chigiriki lomwe limamasuliridwa kuti "kukakamiza".
-
Palibe mutu wofunikira kwambiri kuposa kukhala mu chifuniro cha Mulungu. Chokhacho chomwe chikasiyanitse azitumiki a uthenga ndi kuthekera kwawo kwa kumva mawu a Mulungu molondola. Momwe kulili kwabwino kutsatira Mzimu Woyera ku chifuniro cha Mulungu. Mukakhala mu chifuniro cha Mulungu, muzachita bwino ndipo muzakwaniritsa zokhumba zonse kwa Mulungu. Ntchito yapamwambayi yolembedwa ndi Dag Heward-Mills izakhala ndi kukhudza kwakukulu pa moyo wanu ndi utumiki.
-
Moyo ungakhale wovuta kwa aliyense. Nthawi zambiri chomwe mukufuna kuti mugonjetse chomwe inu mwagwamo ndi nzeru. Nzeru ndi chinsinsi cha Mulungu chomwe chikuthandizeni inu kuwuka kuchokera nkulimbana ndikukhala chozizwitsa chamoyo. Mulungu wakuikani inu ku ulemerero. Chinsinsi cha Mulungu ndi nzeru ya Mulungu mu chinsinsi chomwe chaikidwa pa ulemerero ndi kukongola kwanu. Zibvumbulutso za bukhuli zikubweretsereni chigonjetso tsiku lililonse! Bukhu ili likupatseni chidziwitso ndi kupambana!
-
Bukhuli lizachiza kusweka mitima kwa ana aakazi! Mubukhu loyembekezerekali, akazi akulimbikitsika kulola nzeru ya Mulungu kuwathandiza iwo kugonjetsa zinthu zosatheka zambiri zomwe amakumana nazo. Mulungu adzakhuza moyo wanu ndi kulimbikitsa inu pamene mukulimva bwino bukhu lamphamvu latsopanoli maka maka kwa ana aakazi.
-
Bukhu lija la abusa ndi akazi a abusa lafika! Bukhu ili silikhudza inu ngati sindinu mbusa kapena mkazi wa mbusa! Ngati inu muli oyenerezeka kuwerenga bukuli, muloleni Mulungu akutumikireni inu mu buku loshosha maganizoli. Mu masambawa, maudindo achinsinsi omwe akazi achita mu miyoyo ya azibusa awululika. Masambawa akulangizeni inu ndi kukudzetsani inu m'njira ya mdalisto!
-
Ngati Mkhristu, chikoka chachikulu komanso chokometsetsa mu moyo wanu chikuyenera kukhala Mzimu Woyera. Bukhuli likukulolani kumvetsetsa khalidwe lanu, kuzindikira kwanu, luso lanu ndinso kuthekera kwanu kokhala woyera kutha kukokedwa ndi Mzimu Woyera. Kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, mukuyenera kulola Mzimu Woyera kukukokani, kukulimbikitsani, kukukhadzani komanso kusintha moyo wanu kwa muyaya.
-
Bukhu latsopanoli, "Malamulo a Ntchito ya Mpingo", ndi chida chofunikira kwambiri kwa amene ali ndi chikhumbokhumbo chogwilira ntchito mu tchalitchi. Dag Heward-Mills, mu kalembedwe kake ka nthawi zonse, akupeleka malamulo ogwilira mu utumiki wa nthawi zonse komanso kubweletsa bvumbulutso lofunikira kwambiri pa kuchita bwino mu utumiki.
-
Tonse timalindirira moyo waulemerero komwe kuzakhala "KULIBENSO THEMBERERO!" Ichi ndi chifukwa choti mmoyo timakumana ndi matsoka, kuzunzika kopitirira, utsiru, kusasangalala ndi kukhumudwa. Themberero limafotokoza bwino matsoka okumana nawowa omwe tikuwoneka kuti timakumana nawo. Tingazipewe? Pali njira yosakumanirana nazo? Bukhuli likakuthandizani inu kumvetsetsa matemberero ndi momwe mungazikhadzikitsire nokha kuti mukalandire mdalitso.