-
Dr. Dag Heward-Mills, mtsogoleri wa Chikhristu wopambana, akuonetsa chimodzi mwa zinsinsi zake. “Ngati wina atandifunsa chomwe chinsinsi changa chachikulu cha ubale wanga ndi Mulungu chiri, nditha kunena, musaopa, kuti ndi mphamvu ya nthawi za chete yomwe ndimakhala nayo ndi Iye tsiku ndi tsiku.” Iwe waganiza kulemba bukhuli kuti inunso mukapindule kuchokera ku mphamvu ya nthawi ya chete.
-
Anthu ambiri amavutika ndi lingaliro la kupereka chakhumi ingakhale mchitidwe wakale kalewu wabweretsa chuma kwa Ayuda. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward-Mills akuphunzitsa momwe kupereka chakhumi kumapezera mfundo zikulu zikulu za kupanga chuma ndi zozwizitsa za kuchita bwino. Sangalalani ndi limodzi mwa makope a Dag Heward-Mills.
-
Mutu wa bukhuli likukupangitsani kuganiza pompopompo za ana ang'ono akuyimba mokondwa…Mumawerenga Baibulo lanu tsiku lililonse? Mumapemphera tsiku lililonse?Bukhu ili litsekula maso anu ku bukhu lodabwitsa lapalokha lotchedwa Baibulo. Likutsekuliraninso zozizwa zomwe zimadza kwa inu tsiku lililonse pamene mukuwerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku lililonse. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera kwanu kwa tsiku lililonse kukhale kosangalasa kwa inu!
-
Bukhuli ndi chiongolero chapadera ku kumvetsetsa chipulumutso kudzera mwa Yesu Khristu. Mu bukhu la pamwambali, muzamvetsetsa momwe Yesu amakukonderani inu, momwe mungabadwire mwatsopano, momwe mungapewere kupita ku gehena ndi chomwe chimatanthauza kukhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu. Perekani bukhuli kwa wina aliyense ndipo azamvetsetsa zomwe zikutanthauza kupulumutsidwa kudzera mu mwazi wa Yesu Khristu.
-
Kodi mukudziwa kuti aneneri akale, anafunsa ndi kufufuza zachipulumutso chachikuluchi chomwe chawonetseredwa kwa ife? Iwo sakanaganiza za momwe chipulumutsochi chingabwerere kwa anthu…koma ndife odalitsika kulandira chipulumutsochi! Ife talandira chipulumutso chifukwa winawake adatiuza za ichi. M'bukhu lopatsa chidwili, Mlaliki Dag Heward-Mills akutitsogolera ife kuti tisangomvetsetsa chipulumutso chathu chachikulu komanso mmene tingagawire ena uthenga wabwino wa chipulumutso chachikuluchi. Aliyense mwaife akachite ntchito ya mlaliki!
-
Pamene muyenda mmoyo inu mukapeza kuti dziko lobisika ndi dziko lenileni ndipo dziko lakuthupi ndi chiwonetsero cha zina mwa zinthu zamu dziko lobisika. Monga mmene mulili ndi adani owoneka, inu mulinso ndi adani obisika. Kodi mungamenyane ndi mdani osamudziwa iye, ndondomeko zake, kapangidwe kake ka zinthu ndi zida zake? Bukhu ili ndi chida chofunika ku ulendo wa moyo wanu. M'bukhu ili mukaphunzira kuti adani anu obisika ndi ati, mizu yakukhala kwawo, maonekedwe awo ndi momwe mungapambanire nkhondo ndi iwo. Bukhu labwinoli likuthandizeni kugonjetsa adani anu obisika!
-
Palibe mwaife amene wayika dongosolo lokafika kumwamba opanda kuchita chomwe Mulungu amafuna kuti ife tikachite padziko lapansi. Ayi, olo ndi mmodzi! Ife tikufuna timalize ntchito Mulungu watipatsa ife. Bukhu ili ndilokhudza mmene mungakwanitsire utumiki wanu. Bukhu ili ndi kalondolondo ka momwe ife tingayankhire zochitika zaumulungu mmoyo mwathu - ndicholinga chosafuna kupezeka operewera patsikulo. Mukakwaniritse utumiki wanu ndipo Mulungu akanene kwa inu, "Wachita bwino, kapolo wabwino ndi okhulupirika!"
-
Azibusa ali pa mpani pani wokondweretsa ndi kusangalatsa anthu awo ndi uthenga wabwino. Mpani pani wa anthu umenewu wapangitsa kusintha kwa mawu a Khristu kufikira mawu a mtanda akhalira kovuta kuzindikirika. Lero, tikubwerera ku maziko a chilungamo cha Chikhristu choti tikuyenera “kutaya” kuti “tipeze” Khristu. Mphamvu izabwerera ku mpingo pamene tikulalikira kuti tipereke nsembe, kusautsidwa ndi kufa chifukwa cha Khristu. Mphamvu ya mawu a Khristu siingafufutidwe ndi wina aliyense posatengera kuchita bwino kapena kukhala wa mphamvu.
-
Ingakhale ndi chofunikira choyamba cha Mulungu kwa atsogoleri, zochepa kwambiri zalembedwa pa mutu uwu. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutchula mfundo zikulu zikulu ndi cholinga chokulitsira kukhadzikika kwa matchalitchi. Zamkati mwa bukhuli zili zoyenerera komanso zochitika mpaka ndi kukhala chida chosasiidwa kwa atsogoleri ambiri.
-
Baibulo limayankhula za mitundu yambiri ya mwazi: mwazi wa mbuzi, mwazi wa nkhosa, mwazi wa nkhunda! Baibulo limatiuzanso kuti popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo. Ndiye kodi umodzi mwa mitundu iyi ungather kuchotsa machimo?yankho ndi ‘Ayi’ wotsindika. Ndiye ndi chani chingachotse machimo athu? Palibe, koma mwazi wa Yesu Khristu! Ndi mwazi wa Yesu wokhawo umene uli ndi mphamvu kukachotsa machimo athu ndi kutibweretsera chipulumutso. Mu bukhu lofunikira kwambiri limeri, muzapeza zilungamo zoyera kwambiri zokhuzana ndi mwazi wa Yesu Khristu. Mupeza momwe mwazi wa Yesu umaperekera moyo ndi momwe mwazi wa Yesu unapezera kufunikira kwake. Muzamvetsetsa chiyanjano cha pakati pa Mzimu Woyera ndi mwazi wa Yesu. Mulidi mphamvu mu mwazi wa Yesu!