• Ntchito za ziwanda zaonetsedwa mu bukhu latsopano la pamwambali lolembedwa ndi Dag Heward Mills. Kugwiritsa ntchito umboni wa munthu wamisala wa ku Gadara, akuonetsa njira ya chigonjetso pa ziwanda ndi mizimu yoipa.
  • Mutalandira Yesu Khristu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi wanu mumapulumutsidwa! Inu ndinu Mkhristu wobadwanso mwatsopano ndipo dzina lanu lalembedwa mu Bukhu la Moyo. Funso lanu ndilo: "Kodi sitepe yotsatira ndi yotani?" Pokhala Mkhristu ndi sitepe yabwino, koma ndi chiyambi chabe. Inu mukuyenera kukhala Mkhristu wabwino, wamphamvu. 'Nanga ndichita bwanji izi?' - M'buku ili labwino, mudzaphunzira njira zoti mutenge ndikukhala Mkhristu wamphamvu yemwe ali wokonzeka kufa kapena mkwatulo.
  • Mipingo yadzadzidwa ndi onamizira angwiro amene amakhala osakhulupirika mwangwiro. Chida cheni cheni cha Satana chakhala chinyengo ndi kunamizira. Mtsogoleri amene sazindikira wonyenga azavutika chifukwa cha kusaona kwake.Kuopseza, chizolowezi ndi chisokonezo ndi mizimu yoipa imene imalimbana ndi azitumiki. Nthawi zambiri, anthu samadziwa chomwe chimalimbana nawo. Bukhu ili likakuthandizani inu kudziwa ndi kulimbana ndi mdani wamkati.
  • "Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu. Koma NGATI INU SIMUKHULULUKIRA, ATATE WANU WAKUMWAMBA SAZAKHULULUKIRA INU ZOLAKWA ZANU" (Marko 11:25-26). Kodi ndimezi zikukunjenjemeretsani? Yankho lanu lilipano. Mu bukhu lofunikirali, muphunzira kukhululukira mosavuta - kutinso nanu musangalale ndi chikhululukiro cha Atate wanu wakumwamba. Mulole kuti bukhu ili likhale bwenzi lanu mpaka mutafika poti mukutha kukhululukira mosavuta ndi moona mtima.
  • Anthu opanduka samakumbukira zomwe zapangidwa kwa iwo ndipo nthawi zambiri amasankha kuiwala zinthu zina. Yudase sanakumbukire zimene Ambuye anamchitira, ndinso sanakumbukirenso zinthu zimene anaona ndi kumva kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake adakhala mtundu wa munthu amene tikumudziwa lero ngati ‘Yudase’. Kuthekera kokumbukira ndi chimodzi mwa zinthu zauzimu chomwe mtumiki atha kukhala nacho. Anthu amene samakumbukira, siwamba kuchita bwino. Iwo amalephera kufika mlingo wina. Bukhu lapaderali, pa mutu wosakambidwa kwambiriwu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kwa inu.
  • Mkhristu amayenda mkati kati mwa zoopsa zambiri ndi misampha. Bukhuli likatsekula maso anu ku zoopsa zambiri zobisika zomwe zikudikira kukupwetekani, kuvulaza komanso kuononga. Dzithandizeni nokha, dzipulumutseni nokha kudzera mu bukhu lamphamvu ili la zoopsa zauzimu!
  • Mu bukhu lapamwambali, Bishop Dag Heward-mills amaphunzitsa za momwe chida cha kukhulupirika chimalimbikitsa kachitidwe ka mtsogoleri. Kugwiritsa ntchito baibulo, mbiri ndi zolemba, mutu uwu wapangidwa kukhala woyenera kwa wowerenga.
  • “Ndingapemphere bwanji? Kodi ndipempherere chani? Kodi pemphero ndilodabwitsa chifukwa chani? Ndingapemphere bwanji kwa nthawi yaitali? Kodi Mulungu sakudziwa zomwe ndikufuna? Mapemphero anga ayankhidwadi?” Pezani mayankho a mafunso amenewa pomwe mukuwerenga bukhu lobwera panthawi yake lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Baibulo limatilangiza ife ku: "Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzakeyo" (Afilipi 2:4). M'bukhu la m'nthawi yakeli, Dag Heward-Mills akukuwuzani inu mupitirire kuganiza za inu nokha ndi kuganizanso za ena! Mukondenso ena! Muganizirenso ena! Musamalenso za ena! Mukhalenso chifukwa cha ena! Yesu anadza kudzatifera ife chifukwa Iye anaganiza za "ena". Ine ndikufuna kukhala kwambiri ngati Iye. Kodi inu mukufuna kukhala ngati Yesu?
  • “Mwina mmodzi mwa adani aakulu omwe mutha kukumana nawo ndi ‘woneneza pakati pa abale’.” Landirani chidziwitso chachikulu cha momwe chida chimenechi cha kuneneza chimadzera ndipo phunzirani za momwe mungachigonjetsere, pomwe mukuwerenga bukhu lapamwambali, lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
  • Nthawi zambiri timalimbikitsika pamene tikamaganizira za mfundo yoti “Ambiri Aitanidwa”. Kenako tonse mwachangu timalimbikitsika tikamalingalira za mfundo yoti “…ochepa amasankhidwa.” Mutha kuwerengedwa ndi ambiri amene aitanidwa ndi ochepa amene asankhidwa ngati mupange bukhuli kukhala gawo la moyo wanu.Mu bukhu lodabwitsali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, muzazindikira kuchokera mu Baibulo zifukwa zomwe munganenere motsimikiza kuti ndinu oitanidwa. Inu mudzadziwa za makhalidwe a anthu oitanidwa ndipo muzalimbikitsidwa kukhala wosatekeseka mpaka kumapeto kwa ulendo wanu wa Chikhristu.
  • Anthu amene amakusiya atha kukuwonongani. Palibe chimene chingalongosera kumva kwa kukhumudwa, kubalalika ndi nkhawa zimene zimadza pamene anthu akukusiyani. Bukhu ili lalembedwa kukuthandizani inu kulimbana ndi chiwonongeko chomwe chimadza pamene anthu akusiyani. Musanyengedwe. Kusiidwa sikwachilendo kwa inu ndi utumiki wanu. Ambiri ena avutika ndi zomwezo. Satana anali wopanduka woyamba ndipo akulimbikitsa opandukira onse kuyambira pamenepo. Ndi bukhu limeneri mu manja anu, muzachirimika ndi kulimbana ndi mzimu wa kusakhulupirika umene umadza ndi “iwo amene amakusiyani”.

Title

Go to Top