Dag Heward-Mills ndi wolemba wa mabuku ambiri, kuphatikizapo logulitsidwa kwambiri “Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika”. Ndi woyambitsa wa Mipingo ingapo yochokera ku Lighthose ndi matchalitchi zikwi zitatu.
Dag Heward-Mills, mvangeli wadziko lonse, amatumikira mu misonkhano ya machiritso mu maiko komanso misonkhano ya atsogoleri padziko lonse. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa
www.daghewardmills.org.

  • Nthawi zambiri timalimbikitsika pamene tikamaganizira za mfundo yoti “Ambiri Aitanidwa”. Kenako tonse mwachangu timalimbikitsika tikamalingalira za mfundo yoti “…ochepa amasankhidwa.” Mutha kuwerengedwa ndi ambiri amene aitanidwa ndi ochepa amene asankhidwa ngati mupange bukhuli kukhala gawo la moyo wanu.Mu bukhu lodabwitsali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, muzazindikira kuchokera mu Baibulo zifukwa zomwe munganenere motsimikiza kuti ndinu oitanidwa. Inu mudzadziwa za makhalidwe a anthu oitanidwa ndipo muzalimbikitsidwa kukhala wosatekeseka mpaka kumapeto kwa ulendo wanu wa Chikhristu.
  • N’chifukwa chiyani Mulungu Wamphamvuzonse angafunike munthu? Kodi Ambuye angafunike chiyani kwa iwe? Kodi ndi chiyani chimene Mulungu sangathe kuchita yekha? Kodi ndi chiyani chimene Mulungu sangathe kukwaniritsa yekha? Mulungu akufunafuna munthu amene adzayime pakati pa Iyeyo ndi munthu. Mulungu akufunafuna munthu amene adzayankhe mafunso a ana ang’onoang’ono! Mulungu akufunafuna munthu amene adzafikire ana osatetezedwa! Baibulo limanena kuti Mulungu ankafunafuna munthu…!

    M’mene ukwerenga bukuli lonse, Warmth for the Heart, chikhumbo chako chokhala chombo chofunitsitsa kugwiritsidwa ntchito m’manja a Mulungu chidzaukiridwa. Sudzakhalanso wokhutira kungokhala membala wamba. Udzakhala munthu wothandiza! Udzanena ngati woimba wotchuka uja: “Ambuye, ndikudziwa kuti mukufunikira munthu! Mungandidalire ine!”

  • Anagkazo amatanthauza “kukakamiza”.Amatanthauzanso kupangitsa kuti chifunike, kukusira, ndi kupanikiza mwa njira iliyonse monga kuumiriza, kuwopseza, kukopa ndi kuchonderera. Nthawi zina tiyenera kubwerera ku Chigiriki kuti timvetsetse matanthauzo enieni la mawu ena a M'baibulo. Mukuona, Chipangano Chatsopano chinamasuliridwa kuchokera kuchilankhulo cha Chigiriki ndipo Chipangano Chakale kuchokera ku Chihebri. Anagkazo ndi liwu la Chigiriki lomwe limamasuliridwa kuti "kukakamiza".
  • Minda yayera ndipo kholola la miyoyo lacha, koma alaliki ali kuti? Bukhu lolimbikitsa latsopano la Dag Heward-Mills ndi muitano wachangu kwa Akhristu kukhala otengera miyoyo kwa Khristu.
  • Mu bukhu lapamwambali, Dag Heward-Mills akupereka kuzindikira kwakukulu kwa zochitika m'banja. Bukhu lodabwitsali likagwira ntchito ngati chipangizo chokonzekera kwa phungu wa banja ndi anthu okwatira. Inu mukapeza mu bukhuli, mfundo zotsitsimutsa ndi zosangalatsa zopititsa patsogolo banja lanu. "Bukhu ili ndilodzadza ndi nkhani pa maziko ndi zochitika pa maubwenzi a umunthu mu nthawi imene musanakwatire, muli m'banja ndi ngakhale utatha ukwati. Ili ndi zipangizo zofufuzidwa bwino ndi zovomerezeka pa thunthu ndi kakhalidwe kazolengedwa pazogonana, kubereka kwa anthu, mimba ndi nthawi yobereka ikadutsa. Kuthekera kwa Dotolo Dag Heward-Mills kusintha nkhani zovuta kukhala zophweka ndiye chikhalidwe chosiyanitsa pa bukhuli. Zonse pamodzi, izi zimalipangitsa kukhala bukhu losindikizika lomveka kwambiri, logwiritsika ntchito bwino pa zabanja lero." David Asomani, katswiri wowona za chiberekero cha azimayi. "Bukhu la Bishopu Dag Heward-Mills pa uphungu wa m'banja ndilosowa chifanizo. Maziko ake ngati dotolo wa zachipatala zawonetsedwa momveka bwino mu tsatanetsatane, koma kudzifotokozera kwa zizindikiro zachipatala zomwe zikupangitsa bukhuli kukhala lapadera." Edwin Morgan Ogoe, Mphunzitsi, Sukulu Yaukachenjede ya Ghana, Sukulu Yazachipatala
     
  • M’bukuli lozama komanso lodzaza ndi nzeru, Dag Heward-Mills akufotokoza zimene zidzachitike pa BEMA – mpando woweruzira wa Khristu. Ngakhale kuti machimo athu akhululukidwa, pali chiweruzo chimene chikudikira okhulupirira onse. Chiweruzo chimatengera zimene wachita, zimene zabisika komanso zolinga za zochita zako. Zosankha ndizofunika kwambiri m’moyo. Kusowa kwa chiweruzo kumatanthauza kusowa kwa zosankha! Kusowa kwa chiweruzo kumatsogolera ku chipwirikiti! Luntha la wolemba pakuyankha mafunso ngati, “Kodi chiweruzo ndi chiyani?”, “N’chifukwa chiyani pali chiweruzo?”, komanso chifukwa chake Mulungu amakonda chiweruzo, lidzakutsogolerani kuzindikira kuti chiweruzo ndi chilungamo ndi zinthu zimene ziyenera kuphunzitsidwa, kumveketsedwa ndi kuphunziridwa kuti munthu akhale wokonzeka pa Tsiku la Chiweruzo!
  • Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kucokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda anati, Kuli kuca, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.Yesaya 21:11-12
  • Ambiri ayitanidwa, koma osankhidwa ndi ochepa. (Mateyo 22:14) Ndi choonadi cha moyo kuti anthu ambiri amapatsidwa mwayi waukulu, koma ndi ochepa amene amapindula mokwanira ndi mwayi umenewo. M’Baibulo lonse timaona chitsanzo cha anthu ambiri oyitanidwa koma potsiriza ochepa okha ndi amene amasankhidwa. N’chifukwa chiyani ochepa okha ndi amene amasankhidwa? Funso lakuti n’chifukwa chiyani ochepa okha amasankhidwa ndilo funso lalikulu limene tikufuna kuyankha m’bukuli. Mutatha kuwerenga bukuli losankhidwa bwino lolembedwa ndi wolemba wotchuka Dag Heward-Mills, mudzazindikira mmene zimakhalira kuti anthu ambiri ayitanidwe koma ochepa asankhidwe. Ndikupemphera kuti musatengere mopepuka kuitanidwa kumeneku, komanso mugwire ntchito molimbika kuti mukhale m’modzi mwa ochepa amene amasankhidwa!
  • Anthu ambiri amavutika ndi lingaliro la kupereka chakhumi ingakhale mchitidwe wakale kalewu wabweretsa chuma kwa Ayuda. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward-Mills akuphunzitsa momwe kupereka chakhumi kumapezera mfundo zikulu zikulu za kupanga chuma ndi zozwizitsa za kuchita bwino. Sangalalani ndi limodzi mwa makope a Dag Heward-Mills.
  • Ngati Mkhristu, chikoka chachikulu komanso chokometsetsa mu moyo wanu chikuyenera kukhala Mzimu Woyera. Bukhuli likukulolani kumvetsetsa khalidwe lanu, kuzindikira kwanu, luso lanu ndinso kuthekera kwanu kokhala woyera kutha kukokedwa ndi Mzimu Woyera. Kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, mukuyenera kulola Mzimu Woyera kukukokani, kukulimbikitsani, kukukhadzani komanso kusintha moyo wanu kwa muyaya.
  • Mulungu akufuna kuti anthu onse apulumutsidwe! N'chifukwa chake anatuma Yesu Khristu kuti adzatifere. Yesu adagwiritsa ntchito magazi ake kulipira machimo athu. Ife omwe tapulumutsidwa, Mulungu akutitana kuti tikhale opulumutsa a anthu. Twapatsidwa Lamulo Lalikulu Lotumiza. Mawu omaliza a Yesu kwa ife ndi awa: tipite kudziko lonse lapansi, tikapange ophunzira mwa anthu onse! Kodi udzayankha kuitanidwa kumeneku? Ili ndi mutu wina woyanitsa maganizo m'mndandanda wachikhalidwe wa mabuku a mauthenga a chipulumutso olembedwa ndi Dag Heward-Mills. Mosakayikira, buku ili lidzalimbikitsa wokhulupira aliyense kukwaniritsa udindo wake kwa ochimwa ndi kukhala wopulumutsa wa anthu!
  • Pamene muyenda mmoyo inu mukapeza kuti dziko lobisika ndi dziko lenileni ndipo dziko lakuthupi ndi chiwonetsero cha zina mwa zinthu zamu dziko lobisika. Monga mmene mulili ndi adani owoneka, inu mulinso ndi adani obisika. Kodi mungamenyane ndi mdani osamudziwa iye, ndondomeko zake, kapangidwe kake ka zinthu ndi zida zake? Bukhu ili ndi chida chofunika ku ulendo wa moyo wanu. M'bukhu ili mukaphunzira kuti adani anu obisika ndi ati, mizu yakukhala kwawo, maonekedwe awo ndi momwe mungapambanire nkhondo ndi iwo. Bukhu labwinoli likuthandizeni kugonjetsa adani anu obisika!
     

Title

Go to Top