Dag Heward-Mills ndi wolemba wa mabuku ambiri, kuphatikizapo logulitsidwa kwambiri “Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika”. Ndi woyambitsa wa Mipingo ingapo yochokera ku Lighthose ndi matchalitchi zikwi zitatu.
Dag Heward-Mills, mvangeli wadziko lonse, amatumikira mu misonkhano ya machiritso mu maiko komanso misonkhano ya atsogoleri padziko lonse. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa
www.daghewardmills.org.
-
Nthawi zambiri timalimbikitsika pamene tikamaganizira za mfundo yoti “Ambiri Aitanidwa”. Kenako tonse mwachangu timalimbikitsika tikamalingalira za mfundo yoti “…ochepa amasankhidwa.” Mutha kuwerengedwa ndi ambiri amene aitanidwa ndi ochepa amene asankhidwa ngati mupange bukhuli kukhala gawo la moyo wanu.Mu bukhu lodabwitsali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, muzazindikira kuchokera mu Baibulo zifukwa zomwe munganenere motsimikiza kuti ndinu oitanidwa. Inu mudzadziwa za makhalidwe a anthu oitanidwa ndipo muzalimbikitsidwa kukhala wosatekeseka mpaka kumapeto kwa ulendo wanu wa Chikhristu.
-
Anagkazo amatanthauza “kukakamiza”.Amatanthauzanso kupangitsa kuti chifunike, kukusira, ndi kupanikiza mwa njira iliyonse monga kuumiriza, kuwopseza, kukopa ndi kuchonderera. Nthawi zina tiyenera kubwerera ku Chigiriki kuti timvetsetse matanthauzo enieni la mawu ena a M'baibulo. Mukuona, Chipangano Chatsopano chinamasuliridwa kuchokera kuchilankhulo cha Chigiriki ndipo Chipangano Chakale kuchokera ku Chihebri. Anagkazo ndi liwu la Chigiriki lomwe limamasuliridwa kuti "kukakamiza".
-
Mu bukhu lapamwambali, Dag Heward-Mills akupereka kuzindikira kwakukulu kwa zochitika m'banja. Bukhu lodabwitsali likagwira ntchito ngati chipangizo chokonzekera kwa phungu wa banja ndi anthu okwatira. Inu mukapeza mu bukhuli, mfundo zotsitsimutsa ndi zosangalatsa zopititsa patsogolo banja lanu. "Bukhu ili ndilodzadza ndi nkhani pa maziko ndi zochitika pa maubwenzi a umunthu mu nthawi imene musanakwatire, muli m'banja ndi ngakhale utatha ukwati. Ili ndi zipangizo zofufuzidwa bwino ndi zovomerezeka pa thunthu ndi kakhalidwe kazolengedwa pazogonana, kubereka kwa anthu, mimba ndi nthawi yobereka ikadutsa. Kuthekera kwa Dotolo Dag Heward-Mills kusintha nkhani zovuta kukhala zophweka ndiye chikhalidwe chosiyanitsa pa bukhuli. Zonse pamodzi, izi zimalipangitsa kukhala bukhu losindikizika lomveka kwambiri, logwiritsika ntchito bwino pa zabanja lero." David Asomani, katswiri wowona za chiberekero cha azimayi. "Bukhu la Bishopu Dag Heward-Mills pa uphungu wa m'banja ndilosowa chifanizo. Maziko ake ngati dotolo wa zachipatala zawonetsedwa momveka bwino mu tsatanetsatane, koma kudzifotokozera kwa zizindikiro zachipatala zomwe zikupangitsa bukhuli kukhala lapadera." Edwin Morgan Ogoe, Mphunzitsi, Sukulu Yaukachenjede ya Ghana, Sukulu Yazachipatala
-
Anthu ambiri amavutika ndi lingaliro la kupereka chakhumi ingakhale mchitidwe wakale kalewu wabweretsa chuma kwa Ayuda. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward-Mills akuphunzitsa momwe kupereka chakhumi kumapezera mfundo zikulu zikulu za kupanga chuma ndi zozwizitsa za kuchita bwino. Sangalalani ndi limodzi mwa makope a Dag Heward-Mills.
-
Ngati Mkhristu, chikoka chachikulu komanso chokometsetsa mu moyo wanu chikuyenera kukhala Mzimu Woyera. Bukhuli likukulolani kumvetsetsa khalidwe lanu, kuzindikira kwanu, luso lanu ndinso kuthekera kwanu kokhala woyera kutha kukokedwa ndi Mzimu Woyera. Kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, mukuyenera kulola Mzimu Woyera kukukokani, kukulimbikitsani, kukukhadzani komanso kusintha moyo wanu kwa muyaya.
-
Pamene muyenda mmoyo inu mukapeza kuti dziko lobisika ndi dziko lenileni ndipo dziko lakuthupi ndi chiwonetsero cha zina mwa zinthu zamu dziko lobisika. Monga mmene mulili ndi adani owoneka, inu mulinso ndi adani obisika. Kodi mungamenyane ndi mdani osamudziwa iye, ndondomeko zake, kapangidwe kake ka zinthu ndi zida zake? Bukhu ili ndi chida chofunika ku ulendo wa moyo wanu. M'bukhu ili mukaphunzira kuti adani anu obisika ndi ati, mizu yakukhala kwawo, maonekedwe awo ndi momwe mungapambanire nkhondo ndi iwo. Bukhu labwinoli likuthandizeni kugonjetsa adani anu obisika!
-
Baibulo limatilangiza ife ku: "Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzakeyo" (Afilipi 2:4). M'bukhu la m'nthawi yakeli, Dag Heward-Mills akukuwuzani inu mupitirire kuganiza za inu nokha ndi kuganizanso za ena! Mukondenso ena! Muganizirenso ena! Musamalenso za ena! Mukhalenso chifukwa cha ena! Yesu anadza kudzatifera ife chifukwa Iye anaganiza za "ena". Ine ndikufuna kukhala kwambiri ngati Iye. Kodi inu mukufuna kukhala ngati Yesu?
-
Bukhu iri ndi mphatso ina kuchokera ku cholembera cha Dag Heward-Mills kwa azitumiki onse amene atha kupeza nthawi yowerenga. Bukhuli lizayankha mafunso onse okhuzana ndi momwe mungakwaniritsire kukhala ndi ubale wabwino pakati pa atate ndi ana. Kudzera mu chiphunzitso cha bukhu limeneri, muzapewa themberero pa moyo wanu ndi kubweretsa kwanokha mdalitso. Atate ndi anthu apadera amene amakuza ana. Popanda atate sipazakhala ana kupitiriza utumiki ku mibadwo ina. Maitanidwe a Mulungu amakula kapena kufa ndi kuthekera kochitirana ndi atate. Werengani bukhu limeneri ndipo pewani themberero lokhuzana ndi kusalemekeza, kusamvera ndi kukhala ndi ubale woipa ndi atate.
-
Kudzikweza ndi poizoni wakupha amene waononga mtundu wa anthu mzaka zambiri. Chifukwa nkosatheka, kudzikweza kumakwaniritsa kupangitsa chionongeko chachikulu popanda kuonekera. Tingamenyane bwanji ndi chiopsezo chimenechi ku miyoyo yathu? Ndi katemera wa kudzichepetsa! Kudzichepetsa ndi chabwino chauzimu. Ochepa akwanitsa kulemba zokhudzana ndi chofunikira chauzimuchi. Mu bukhu latsopano losangalatsali, Dag Heward-Mills akuonetsera mitundi yobisika ya kudzikweza. Bukhu la mphamvu limeneri, lolembedwa ndi Mkhristu wovutika mzathu, likudalitsani ndi kukulimbikitsani inu kukuza kudzichepetsa konga mwana kwa Yesu Khristu.
-
Anthu opanduka samakumbukira zomwe zapangidwa kwa iwo ndipo nthawi zambiri amasankha kuiwala zinthu zina. Yudase sanakumbukire zimene Ambuye anamchitira, ndinso sanakumbukirenso zinthu zimene anaona ndi kumva kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake adakhala mtundu wa munthu amene tikumudziwa lero ngati ‘Yudase’. Kuthekera kokumbukira ndi chimodzi mwa zinthu zauzimu chomwe mtumiki atha kukhala nacho. Anthu amene samakumbukira, siwamba kuchita bwino. Iwo amalephera kufika mlingo wina. Bukhu lapaderali, pa mutu wosakambidwa kwambiriwu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kwa inu.
-
Anthu amene amakusiya atha kukuwonongani. Palibe chimene chingalongosera kumva kwa kukhumudwa, kubalalika ndi nkhawa zimene zimadza pamene anthu akukusiyani. Bukhu ili lalembedwa kukuthandizani inu kulimbana ndi chiwonongeko chomwe chimadza pamene anthu akusiyani. Musanyengedwe. Kusiidwa sikwachilendo kwa inu ndi utumiki wanu. Ambiri ena avutika ndi zomwezo. Satana anali wopanduka woyamba ndipo akulimbikitsa opandukira onse kuyambira pamenepo. Ndi bukhu limeneri mu manja anu, muzachirimika ndi kulimbana ndi mzimu wa kusakhulupirika umene umadza ndi “iwo amene amakusiyani”.
-
Mipingo yadzadzidwa ndi onamizira angwiro amene amakhala osakhulupirika mwangwiro. Chida cheni cheni cha Satana chakhala chinyengo ndi kunamizira. Mtsogoleri amene sazindikira wonyenga azavutika chifukwa cha kusaona kwake.Kuopseza, chizolowezi ndi chisokonezo ndi mizimu yoipa imene imalimbana ndi azitumiki. Nthawi zambiri, anthu samadziwa chomwe chimalimbana nawo. Bukhu ili likakuthandizani inu kudziwa ndi kulimbana ndi mdani wamkati.
-
Yesu Khristu akuonetsera mfundo yodabwitsa yomwe ikutsogolera kuchita bwino ndi chuma. Iye amene ali nako kanthu azakhala nazo zambiri! Zikumveka mokondera! Koma, ichi ndi chilungamo chomwe chikuonetsedwa kwa ife tsiku ndi tsiku. Bukhuli likulongosola Lemba losamvetsetseka kwambiri iri. Muzalandira chidziwitso chachikulu ku zinsinsi za kuchita bwino pamene mukuwerenga bukhu latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills.
-
Kubzala mipingo ndi chinthu chomwe chafalikira pakati pa azitumiki a uthenga wabwino. Inali ntchito ya ophunzira oyambirira. Kubzala mipingo kopambana kumafuna luso ndi zina zambiri. Dag Heward-Mills, woyambitsa matchalitchi zikwi zitatu padziko lonse, akutitsogolera ife kuunikira zinthu zosiyana siyana za kubzala mpingo mu bukhuli. Ili ndi kope la kuphunzirirapo kwa mtumiki ali yense amene akufuna kupanga kubzala mipingo kukhala masomphenya ake a moyo ndi utumiki.
-
"Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu. Koma NGATI INU SIMUKHULULUKIRA, ATATE WANU WAKUMWAMBA SAZAKHULULUKIRA INU ZOLAKWA ZANU" (Marko 11:25-26). Kodi ndimezi zikukunjenjemeretsani? Yankho lanu lilipano. Mu bukhu lofunikirali, muphunzira kukhululukira mosavuta - kutinso nanu musangalale ndi chikhululukiro cha Atate wanu wakumwamba. Mulole kuti bukhu ili likhale bwenzi lanu mpaka mutafika poti mukutha kukhululukira mosavuta ndi moona mtima.
-
Ingakhale ndi chofunikira choyamba cha Mulungu kwa atsogoleri, zochepa kwambiri zalembedwa pa mutu uwu. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutchula mfundo zikulu zikulu ndi cholinga chokulitsira kukhadzikika kwa matchalitchi. Zamkati mwa bukhuli zili zoyenerera komanso zochitika mpaka ndi kukhala chida chosasiidwa kwa atsogoleri ambiri.
-
Bukhu lija la abusa ndi akazi a abusa lafika! Bukhu ili silikhudza inu ngati sindinu mbusa kapena mkazi wa mbusa! Ngati inu muli oyenerezeka kuwerenga bukuli, muloleni Mulungu akutumikireni inu mu buku loshosha maganizoli. Mu masambawa, maudindo achinsinsi omwe akazi achita mu miyoyo ya azibusa awululika. Masambawa akulangizeni inu ndi kukudzetsani inu m'njira ya mdalisto!
-
Tikudziwa kui kukula kwa mpingo ndi chinthu chovuta kukwaniritsa. azibusa onse amafuna mpingo wawo ukule. bukhuli ndi yankho la kufuna kwanu kwa kukula kwa mpingo. mukamvetsetsa momwe "zinthu zosiyanasiyana zimawirira pamodzi" kukwaniritsa kukula kwa mpingo. wokondedwa m'busa, pomwe mawu ndi kudzoza kuli m'bukhuli kukubwera mu mtima mwanu, muzakhala ndi kukula kwa mpingo komwe mwakhala mukupempherera.
-
Kudzoza ndi chifungulo chachichikulu chofunikira kutsegula khomo la kuchita bwino ndo kukwaniritsa utumiki. Anthu ambiri ayesera kuchita ntchito ya Mulungu chifukwa cha mafuno abwino, popanda kufika kutali analephera kuzindikira kuti “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu Wanga (Kudzoza)” [Zekariya 4:4]. Bukhu lapderali “Kupeza Kudzoza” lolembedwa ndi Bishopu Dag Heward-mills lizakuphunzitsani inu zomwe zimatanthauza kupeza kudzoza ndi momwe mungapangire! Lolani chikhumbo khumbo cha Kudzoza kwa Mulungu kutakasike mkati mwanu kudzera mu masamba a m’bukhuli!
-
Azibusa ali pa mpani pani wokondweretsa ndi kusangalatsa anthu awo ndi uthenga wabwino. Mpani pani wa anthu umenewu wapangitsa kusintha kwa mawu a Khristu kufikira mawu a mtanda akhalira kovuta kuzindikirika. Lero, tikubwerera ku maziko a chilungamo cha Chikhristu choti tikuyenera “kutaya” kuti “tipeze” Khristu. Mphamvu izabwerera ku mpingo pamene tikulalikira kuti tipereke nsembe, kusautsidwa ndi kufa chifukwa cha Khristu. Mphamvu ya mawu a Khristu siingafufutidwe ndi wina aliyense posatengera kuchita bwino kapena kukhala wa mphamvu.
-
Mawu a Chigiriki akuti LAIKOS akutanthauza “kupanda luso”. Mbiri yatiphunzitsa kwa nthawi ndi nthawi kuti zinthu zazikulu zakwaniritsidwa kudzera kwa anthu amene “anasowekera luso”. Phunzirani, kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, zomwe zimachitika pamene palibe anthu a wamba kugwira ntchito mu tchalitchi; momwe mungagawanirane zolemetsa ndi anthu wamba ndi momwe tikuyenera kulimbanira kuteteza utumiki wa wamba.
-
Palibe mutu wofunikira kwambiri kuposa kukhala mu chifuniro cha Mulungu. Chokhacho chomwe chikasiyanitse azitumiki a uthenga ndi kuthekera kwawo kwa kumva mawu a Mulungu molondola. Momwe kulili kwabwino kutsatira Mzimu Woyera ku chifuniro cha Mulungu. Mukakhala mu chifuniro cha Mulungu, muzachita bwino ndipo muzakwaniritsa zokhumba zonse kwa Mulungu. Ntchito yapamwambayi yolembedwa ndi Dag Heward-Mills izakhala ndi kukhudza kwakukulu pa moyo wanu ndi utumiki.
-
Kutsatira Mulungu ndi ulendo wosangalatsa wopeza zinthu. Kutsatira ndi kutengera anthu ena ndi luso lachikale lophunzirira lomwe Yesu Khristu anasankha ngati njira yaikulu yophunzitsira. M’malo mochita manyazi ndi njira yoyesedwa ndi nthawiyi, ndi nthawi yomvetsetsa kukongola ndi kudzichepetsa kwa luso la kutsatira. Mu bukhuli, muzapeza yemwe, chomwe ndi momwe mungatsatire moyenerera. Bukhu lopambana latsopanoli lolembedwa ndi Dag Heward-Mills lipereka luso la kutsatira malo ake oyenerera mu zokumana zathu za Chikhristu.
-
Ngati ndinu m’busa wa nkhosa za Mulungu, muzathandizika kwambiri ndi ntchito yabwinoyi. Masamba amenewa ali ndi malangizo ofotokozedwa bwino, ofunikira pa kuchita bwino kwanu. Bishop Dag Heward-Mills akutenga kuchokera mukukhala kwake kwa zaka zoposera makumi atatu ngati m’busa, kugawana nafe zinthu zochita mu ntchio ya utumiki. Ngati mwasirira kukhala m’busa wa anthu a Mulungu, iri ndi bukhu lokutsogolerani lomwe mwakhala mukulifuna.
-
Palibe mwaife amene wayika dongosolo lokafika kumwamba opanda kuchita chomwe Mulungu amafuna kuti ife tikachite padziko lapansi. Ayi, olo ndi mmodzi! Ife tikufuna timalize ntchito Mulungu watipatsa ife. Bukhu ili ndilokhudza mmene mungakwanitsire utumiki wanu. Bukhu ili ndi kalondolondo ka momwe ife tingayankhire zochitika zaumulungu mmoyo mwathu - ndicholinga chosafuna kupezeka operewera patsikulo. Mukakwaniritse utumiki wanu ndipo Mulungu akanene kwa inu, "Wachita bwino, kapolo wabwino ndi okhulupirika!"
-
Kodi mukudziwa kuti aneneri akale, anafunsa ndi kufufuza zachipulumutso chachikuluchi chomwe chawonetseredwa kwa ife? Iwo sakanaganiza za momwe chipulumutsochi chingabwerere kwa anthu…koma ndife odalitsika kulandira chipulumutsochi! Ife talandira chipulumutso chifukwa winawake adatiuza za ichi. M'bukhu lopatsa chidwili, Mlaliki Dag Heward-Mills akutitsogolera ife kuti tisangomvetsetsa chipulumutso chathu chachikulu komanso mmene tingagawire ena uthenga wabwino wa chipulumutso chachikuluchi. Aliyense mwaife akachite ntchito ya mlaliki!
-
Bukhu latsopanoli, "Malamulo a Ntchito ya Mpingo", ndi chida chofunikira kwambiri kwa amene ali ndi chikhumbokhumbo chogwilira ntchito mu tchalitchi. Dag Heward-Mills, mu kalembedwe kake ka nthawi zonse, akupeleka malamulo ogwilira mu utumiki wa nthawi zonse komanso kubweletsa bvumbulutso lofunikira kwambiri pa kuchita bwino mu utumiki.
-
Bukhu limeneri ndi chotsatira chomwe chadikiridwa kwambiri cha “M’busa Wamba ndi Utumiki”. Kumaimira kusiyana kwa pakati pa utumiki wa munthu wamba ndi utumiki wa nthawi zonse. Mu bukhu lapaderali Dag Heward-Mills akukulimbikitsani kuti mukadzipereke nokha kwa thunthu kwa Mulungu ndi kukupangitsani kupeza zifukwa zoyenera zolowera mu utumiki wa nthawi zonse.
-
Mutalandira Yesu Khristu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi wanu mumapulumutsidwa! Inu ndinu Mkhristu wobadwanso mwatsopano ndipo dzina lanu lalembedwa mu Bukhu la Moyo. Funso lanu ndilo: "Kodi sitepe yotsatira ndi yotani?" Pokhala Mkhristu ndi sitepe yabwino, koma ndi chiyambi chabe. Inu mukuyenera kukhala Mkhristu wabwino, wamphamvu. 'Nanga ndichita bwanji izi?' - M'buku ili labwino, mudzaphunzira njira zoti mutenge ndikukhala Mkhristu wamphamvu yemwe ali wokonzeka kufa kapena mkwatulo.