-
Mutu wa bukhuli likukupangitsani kuganiza pompopompo za ana ang'ono akuyimba mokondwa…Mumawerenga Baibulo lanu tsiku lililonse? Mumapemphera tsiku lililonse?Bukhu ili litsekula maso anu ku bukhu lodabwitsa lapalokha lotchedwa Baibulo. Likutsekuliraninso zozizwa zomwe zimadza kwa inu tsiku lililonse pamene mukuwerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku lililonse. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera kwanu kwa tsiku lililonse kukhale kosangalasa kwa inu!
-
Moyo ungakhale wovuta kwa aliyense. Nthawi zambiri chomwe mukufuna kuti mugonjetse chomwe inu mwagwamo ndi nzeru. Nzeru ndi chinsinsi cha Mulungu chomwe chikuthandizeni inu kuwuka kuchokera nkulimbana ndikukhala chozizwitsa chamoyo. Mulungu wakuikani inu ku ulemerero. Chinsinsi cha Mulungu ndi nzeru ya Mulungu mu chinsinsi chomwe chaikidwa pa ulemerero ndi kukongola kwanu. Zibvumbulutso za bukhuli zikubweretsereni chigonjetso tsiku lililonse! Bukhu ili likupatseni chidziwitso ndi kupambana!
-
Kodi Chimachitika Ndi Chiyani Mukabadwa Mwatsopano? Mzimu wa Mulungu azabwera pa inu, komanso mumtima mwanu. Kenako mkati mwanu mudzabadwa kapena kupangidwanso. Mulungu amakupatsani mtima watsopano ndi mzimu zonse! Ndi mzimu wanu watsopano, mumakhala munthu watsopano kapena cholengedwa chatsopano. Mwakonzeka kukhala moyo watsopano. Moyo watsopanowu ndiwotheka chifukwa ndiwe munthu watsopano wamtima watsopano. Kubadwa mwatsopano ndikosavuta monga choncho. Anthu amafuna kuchita zinthu zovuta. Koma kubadwanso mwatsopano ndikosavuta!
-
Baibulo limatiuza kuti tonse timalakwitsa- Abusa nawo amalakwitsanso. Kulakwitsa kumabwezeretsa m’mbuyo. Kulakwitsa kumalepheretsa kupita chitsogolo. Kodi ndi zolakwitsa ziti zimene abusa anu apanga? Kodi ndi chiyani chingakhale zolakwitsa zazikulu khumi zimene abusa amachita? Muli omasuka kuwerenga Bukuli ndi kuzindikira zolakwika zimene mungazichite ndi m'mene mungazipewere. Buku lofunikali lidzakhala mdalitso kwa inu ndi utumiki wanu.
-
Chinthu chimodzi chokha chimadza kwa inu mukamva mawu akuti "M’busa" - nkhosa! Nkhosa ndi nyama zodalira zome zimafunikira abusa. M’busa ndi wotsogolera wosamalira komanso wachikondi kwa nkhosa. M'Baibulo, Mulungu amatitchula ife ngati gulu la nkhosa za Mulungu. Yesu adamuuza wophunzira Petro kuti adyetse nkhosa zake kuti atsimikizire za chikondi chake cha Mpulumutsi. Kukhala m'busa ndi ntchito yabwino kwambiri. Ndi chinthu chapamwamba kuitanidwa ndi Mulungu ndi kulembetsedwa mwa antchito Ake ndi kusamalira nkhosa. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutiitanira ife, akutilimbikitsa ndi kutiwonetsa ife momwe tingatengerepo nawo mbali pa ntchito yayikulu yosamalira anthu a Mulungu. Musati muzisiyidwe kunja kwa ntchito yabwino iyi yokhala m’busa!