• Mkhristu amayenda mkati kati mwa zoopsa zambiri ndi misampha. Bukhuli likatsekula maso anu ku zoopsa zambiri zobisika zomwe zikudikira kukupwetekani, kuvulaza komanso kuononga. Dzithandizeni nokha, dzipulumutseni nokha kudzera mu bukhu lamphamvu ili la zoopsa zauzimu!
  • Anthu opanduka samakumbukira zomwe zapangidwa kwa iwo ndipo nthawi zambiri amasankha kuiwala zinthu zina. Yudase sanakumbukire zimene Ambuye anamchitira, ndinso sanakumbukirenso zinthu zimene anaona ndi kumva kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake adakhala mtundu wa munthu amene tikumudziwa lero ngati ‘Yudase’. Kuthekera kokumbukira ndi chimodzi mwa zinthu zauzimu chomwe mtumiki atha kukhala nacho. Anthu amene samakumbukira, siwamba kuchita bwino. Iwo amalephera kufika mlingo wina. Bukhu lapaderali, pa mutu wosakambidwa kwambiriwu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kwa inu.
  • "Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu. Koma NGATI INU SIMUKHULULUKIRA, ATATE WANU WAKUMWAMBA SAZAKHULULUKIRA INU ZOLAKWA ZANU" (Marko 11:25-26). Kodi ndimezi zikukunjenjemeretsani? Yankho lanu lilipano. Mu bukhu lofunikirali, muphunzira kukhululukira mosavuta - kutinso nanu musangalale ndi chikhululukiro cha Atate wanu wakumwamba. Mulole kuti bukhu ili likhale bwenzi lanu mpaka mutafika poti mukutha kukhululukira mosavuta ndi moona mtima.
  • Mipingo yadzadzidwa ndi onamizira angwiro amene amakhala osakhulupirika mwangwiro. Chida cheni cheni cha Satana chakhala chinyengo ndi kunamizira. Mtsogoleri amene sazindikira wonyenga azavutika chifukwa cha kusaona kwake.Kuopseza, chizolowezi ndi chisokonezo ndi mizimu yoipa imene imalimbana ndi azitumiki. Nthawi zambiri, anthu samadziwa chomwe chimalimbana nawo. Bukhu ili likakuthandizani inu kudziwa ndi kulimbana ndi mdani wamkati.
  • Mutalandira Yesu Khristu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi wanu mumapulumutsidwa! Inu ndinu Mkhristu wobadwanso mwatsopano ndipo dzina lanu lalembedwa mu Bukhu la Moyo. Funso lanu ndilo: "Kodi sitepe yotsatira ndi yotani?" Pokhala Mkhristu ndi sitepe yabwino, koma ndi chiyambi chabe. Inu mukuyenera kukhala Mkhristu wabwino, wamphamvu. 'Nanga ndichita bwanji izi?' - M'buku ili labwino, mudzaphunzira njira zoti mutenge ndikukhala Mkhristu wamphamvu yemwe ali wokonzeka kufa kapena mkwatulo.
  • Ntchito za ziwanda zaonetsedwa mu bukhu latsopano la pamwambali lolembedwa ndi Dag Heward Mills. Kugwiritsa ntchito umboni wa munthu wamisala wa ku Gadara, akuonetsa njira ya chigonjetso pa ziwanda ndi mizimu yoipa.
  • Baibulo limayankhula za mitundu yambiri ya mwazi: mwazi wa mbuzi, mwazi wa nkhosa, mwazi wa nkhunda! Baibulo limatiuzanso kuti popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo. Ndiye kodi umodzi mwa mitundu iyi ungather kuchotsa machimo?yankho ndi ‘Ayi’ wotsindika. Ndiye ndi chani chingachotse machimo athu? Palibe, koma mwazi wa Yesu Khristu! Ndi mwazi wa Yesu wokhawo umene uli ndi mphamvu kukachotsa machimo athu ndi kutibweretsera chipulumutso. Mu bukhu lofunikira kwambiri limeri, muzapeza zilungamo zoyera kwambiri zokhuzana ndi mwazi wa Yesu Khristu. Mupeza momwe mwazi wa Yesu umaperekera moyo ndi momwe mwazi wa Yesu unapezera kufunikira kwake. Muzamvetsetsa chiyanjano cha pakati pa Mzimu Woyera ndi mwazi wa Yesu. Mulidi mphamvu mu mwazi wa Yesu!
  • Ingakhale ndi chofunikira choyamba cha Mulungu kwa atsogoleri, zochepa kwambiri zalembedwa pa mutu uwu. Mu bukhuli, Dag Heward-Mills akutchula mfundo zikulu zikulu ndi cholinga chokulitsira kukhadzikika kwa matchalitchi. Zamkati mwa bukhuli zili zoyenerera komanso zochitika mpaka ndi kukhala chida chosasiidwa kwa atsogoleri ambiri.
  • Azibusa ali pa mpani pani wokondweretsa ndi kusangalatsa anthu awo ndi uthenga wabwino. Mpani pani wa anthu umenewu wapangitsa kusintha kwa mawu a Khristu kufikira mawu a mtanda akhalira kovuta kuzindikirika. Lero, tikubwerera ku maziko a chilungamo cha Chikhristu choti tikuyenera “kutaya” kuti “tipeze” Khristu. Mphamvu izabwerera ku mpingo pamene tikulalikira kuti tipereke nsembe, kusautsidwa ndi kufa chifukwa cha Khristu. Mphamvu ya mawu a Khristu siingafufutidwe ndi wina aliyense posatengera kuchita bwino kapena kukhala wa mphamvu.
  • Palibe mwaife amene wayika dongosolo lokafika kumwamba opanda kuchita chomwe Mulungu amafuna kuti ife tikachite padziko lapansi. Ayi, olo ndi mmodzi! Ife tikufuna timalize ntchito Mulungu watipatsa ife. Bukhu ili ndilokhudza mmene mungakwanitsire utumiki wanu. Bukhu ili ndi kalondolondo ka momwe ife tingayankhire zochitika zaumulungu mmoyo mwathu - ndicholinga chosafuna kupezeka operewera patsikulo. Mukakwaniritse utumiki wanu ndipo Mulungu akanene kwa inu, "Wachita bwino, kapolo wabwino ndi okhulupirika!"
  • Yesu anati: mukhale ochenjera ngati njoka ndi oona mtima ngati nkhunda. Kodi njoka ndizochenjeradi? Nchifukwa chiyani Yesu angapereke langizo ngati limeneli? Tengani kaulendo mu bukhu lopangitsa chidwiri la Dag Heward-Mills, ndi kuzipezera nzeru zobisika za njoka.
  • Pamene muyenda mmoyo inu mukapeza kuti dziko lobisika ndi dziko lenileni ndipo dziko lakuthupi ndi chiwonetsero cha zina mwa zinthu zamu dziko lobisika. Monga mmene mulili ndi adani owoneka, inu mulinso ndi adani obisika. Kodi mungamenyane ndi mdani osamudziwa iye, ndondomeko zake, kapangidwe kake ka zinthu ndi zida zake? Bukhu ili ndi chida chofunika ku ulendo wa moyo wanu. M'bukhu ili mukaphunzira kuti adani anu obisika ndi ati, mizu yakukhala kwawo, maonekedwe awo ndi momwe mungapambanire nkhondo ndi iwo. Bukhu labwinoli likuthandizeni kugonjetsa adani anu obisika!
     

Title

Go to Top